Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Danieli 11:2 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 “Ndipo tsopano ndikuwuza zoona: Mafumu ena atatu adzalamulira ku Peresiya, ndipo kenaka padzadzuka mfumu yachinayi imene idzakhala yolemera kwambiri kuposa onsewo. Popeza kuti idzakhala ndi mphamvu chifukwa cha chuma chake, idzadzutsa onse kuti alimbane ndi ufumu wa Grisi.

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

2 Ndipo tsopano ndikufotokozera choonadi. Taona, adzaukanso mafumu atatu mu Persiya, ndi yachinai idzakhala yolemera ndithu yoposa onsewo; ndipo itadzilimbitsa yokha mwa kulemera kwake idzawautsa onse alimbane nao ufumu wa Agriki.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 Ndipo tsopano ndikufotokozera choonadi. Taona, adzaukanso mafumu atatu m'Persiya, ndi yachinai idzakhala yolemera ndithu yoposa onsewo; ndipo itadzilimbitsa yokha mwa kulemera kwake idzawautsa onse alimbane nao ufumu wa Agriki.

Onani mutuwo Koperani




Danieli 11:2
17 Mawu Ofanana  

Motero ntchito yomanga Nyumba ya Mulungu ku Yerusalemu inayimitsidwa mpaka chaka cha chiwiri cha ulamuliro wa Dariyo mfumu ya ku Perisiya.


Ndiponso mʼnthawi ya Aritasasita mfumu ya Perisiya, Bisilamu, Mitiredati, Tabeeli ndi anzawo ena analemba kalata inanso kwa Aritasasita. Kalatayo inalembedwa mʼChiaramu ndipo ankatanthauzira poyiwerenga.


Izi ndi zimene zinachitika pa nthawi ya ufumu wa Ahasiwero, amene analamulira zigawo 127 kuyambira ku India mpaka ku Kusi.


malangizo okudziwitsa zolungama ndi zoona ndi kuti ukawayankhe zoona amene akutumawo?


Chaka chachitatu cha Koresi mfumu ya Aperezi, Danieli amene ankatchedwa Belitesezara analandira mawu a vumbulutso. Uthenga wake unali woona ndipo anawumvetsa movutikira. Uthengawu anawumva kudzera mʼmasomphenya.


“Mfumu ya kumpoto idzalimba mtima, ndipo idzasonkhanitsa gulu lalikulu la ankhondo kuti lithire nkhondo mfumu yakummwera. Mfumu yakummwera ndi gulu lake lankhondo lalikulu ndi lamphamvu idzathirana nkhondo ndi mfumu yakumpoto koma sidzapambana chifukwa cha ziwembu zimene adzamukonzera.


“Ndipo ndinaona chirombo chachiwiri, chimene chimaoneka ngati chimbalangondo. Chinali chonyamuka mbali imodzi, ndipo chinapana nthiti zitatu mʼkamwa mwake pakati pa mano ake. Anachilamula kuti, ‘Nyamuka, idya nyama yambiri!’


Mbuzi yayimuna ija ndi mfumu ya Agriki, ndipo nyanga yayikulu pakati pa maso ake aja ndi mfumu yoyamba.


“Masomphenya okhudza madzulo ndi mmawa amene unawaona aja ndi woona, koma uwasunge masomphenyawa mwachinsinsi popeza ndi onena za masiku a mʼtsogolo kwambiri.”


Ndinaona nkhosa yayimunayo ikuthamanga mwaukali kupita kumadzulo, kumpoto ndi kummwera. Palibe chirombo chimene chikanatha kulimbana nayo, ndipo palibe akanatha kulanditsa kanthu kwa iyo. Iyo inachita monga inafunira ndipo inali ndi mphamvu zambiri.


Zoonadi Ambuye Yehova sachita kanthu asanawulule zimene akufuna kuchita kwa atumiki ake, aneneri.


Ngati anawatcha milungu anthu amene analandira mawu a Mulungu, pajatu Malemba sangasweke,


Amene anakhala pa mpando waufumuyo anati, “Ndikulenga zinthu zonse zikhale zatsopano!” Ndipo anati, “Lemba izi, pakuti mawu awa ndi okhulupirika ndi woona.”


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa