Ndipo kunali, pakumva mau awa, ndinakhala pansi ndi kulira misozi, ndi kuchita maliro masiku ena, ndinasalanso, ndi kupemphera pamaso pa Mulungu wa Kumwamba,
Danieli 10:2 - Buku Lopatulika Masiku aja ine Daniele ndinali kulira masabata atatu amphumphu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Masiku aja ine Daniele ndinali kulira masabata atatu amphumphu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pa nthawi imeneyi, ine Danieli ndinalira kwa masabata atatu. |
Ndipo kunali, pakumva mau awa, ndinakhala pansi ndi kulira misozi, ndi kuchita maliro masiku ena, ndinasalanso, ndi kupemphera pamaso pa Mulungu wa Kumwamba,
Ndidzati kwa Mulungu, thanthwe langa, mwandiiwala chifukwa ninji? Ndimayenderanji wakulira chifukwa cha kundipsinja mdaniyo?
Pakuti Inu ndinu Mulungu wa mphamvu yanga; mwanditayiranji? Ndimayenderanji woliralira chifukwa cha kundipsinja mdani?
Sangalalani inu pamodzi ndi Yerusalemu, ndipo kondwani chifukwa cha iye, inu nonse amene mumkonda; sangalalani kokondwa pamodzi ndi iye, inu nonse akumlira maliro;
Ha, mutu wanga ukadakhala madzi, ndi maso anga kasupe wa misozi, kuti usana ndi usiku ndilirire ophedwa a mwana wamkazi wa anthu anga!
Pamenepo anati kwa ine, Usaope Daniele; pakuti kuyambira tsiku loyamba lija unaika mtima wako kuzindikira ndi kudzichepetsa pamaso pa Mulungu wako, mau ako anamveka; ndipo ndadzera mau ako.
Ndipo Yesu anati kwa iwo, Nanga anyamata a nyumba ya ukwati angathe kulira kodi nthawi imene mkwati akhala nao? Koma adzafika masiku, pamene mkwati adzachotsedwa kwa iwo, ndipo pomwepo adzasala kudya.
Khalani osautsidwa, lirani, lirani misozi; kuseka kwanu kusanduke kulira, ndi chimwemwe chanu chisanduke chisoni.
Ndipo wina akafuna kuipsa izo, moto utuluka m'kamwa mwao, nuononga adani ao; ndipo wina akafuna kuipsa izo, maphedwe ake ayenera kutero.