Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Chivumbulutso 11:5 - Buku Lopatulika

5 Ndipo wina akafuna kuipsa izo, moto utuluka m'kamwa mwao, nuononga adani ao; ndipo wina akafuna kuipsa izo, maphedwe ake ayenera kutero.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

5 Ndipo wina akafuna kuipsa izo, moto utuluka m'kamwa mwao, nuononga adani ao; ndipo wina akafuna kuipsa izo, maphedwe ake ayenera kutero.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

5 Wina aliyense akafuna kuzipweteka mbonizo, moto umatuluka kukamwa kwao nkuwononga adani aowo. Ndipo munthu aliyense wofuna kuzipweteka, adzayenera kuphedwa mwa njira yomweyo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

5 Ngati wina atafuna kuzipweteka mbonizo, moto umatuluka mʼkamwa mwawo ndikuwononga adani awo.

Onani mutuwo Koperani




Chivumbulutso 11:5
13 Mawu Ofanana  

Unakwera utsi wotuluka m'mphuno mwake, ndi moto wa m'kamwa mwake unanyeka nuyakitsa makala.


koma ndi chilungamo adzaweruza aumphawi, nadzadzudzulira ofatsa a m'dziko moongoka; ndipo adzamenya dziko lapansi ndi chibonga cha kukamwa kwake, nadzapha oipa ndi mpweya wa milomo yake.


penyatu, lero ndakuika ulamulire mitundu ya anthu ndi maufumu, kuti uzule, upasule, uononge, ugwetse, umange, ubzale.


Chifukwa chake Yehova Mulungu wa makamu atero, Chifukwa munena mau awa, taona, ndidzayesa mau anga akhale m'kamwa mwako ngati moto, anthu awa ndidzayesa nkhuni, ndipo udzawatha iwo.


Ndipo maonekedwe a masomphenya ndinawaona anali monga masomphenya aja ndinawaona pakudza ine kupasula mzinda; ndi masomphenyawa anali ngati masomphenya aja ndinawaona kumtsinje wa Kebara; ndipo ndinagwa nkhope pansi.


Chifukwa chake ndawalikha mwa aneneri; ndawapha ndi mau a pakamwa panga; ndi maweruzo anga atuluka ngati kuunika.


Koma mau anga ndi malemba anga, amene ndinalamulira atumiki anga aneneriwo, kodi sanawapeze makolo anu? Ndipo anabwera, nati, Monga umo Yehova wa makamu analingirira kutichitira ife, monga mwa njira zathu ndi monga mwa machitidwe athu, momwemo anatichitira.


Pakuti atero Yehova wa makamu: Utatha ulemererowo ananditumiza kwa amitundu amene anakufunkhani; pakuti iye wokhudza inu, akhudza mwana wa m'diso lake.


Ndipo chichita zizindikiro zazikulu, kutinso chitsitse moto uchokere m'mwamba nugwe padziko, pamaso pa anthu.


Ndipo kotero ndinaona akavalo m'masomphenya, ndi iwo akuwakwera akukhala nazo zikopa za moto, ndi huakinto ndi sulufure; ndi mitu ya akavalo ngati mitu ya mikango; ndipo m'kamwa mwao mutuluka moto ndi utsi ndi sulufure.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa