Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 43:2 - Buku Lopatulika

2 Pakuti Inu ndinu Mulungu wa mphamvu yanga; mwanditayiranji? Ndimayenderanji woliralira chifukwa cha kundipsinja mdani?

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 Pakuti Inu ndinu Mulungu wa mphamvu yanga; mwanditayiranji? Ndimayenderanji woliralira chifukwa cha kundipsinja mdani?

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

2 Ndithu Inu ndinu Mulungu wamphamvu amene ndimathaŵirako. Mwanditayiranji? Ndiziyenderanji ndilikulira chifukwa chondipsinja mdani wanga?

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Pajatu Inu Mulungu ndinu mphamvu zanga. Nʼchifukwa chiyani mwandikana ine? Nʼchifukwa chiyani ndiyenera kuyenda ndikulira, woponderezedwa ndi mdani?

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 43:2
17 Mawu Ofanana  

Ndipo iwe Solomoni mwana wanga, umdziwe Mulungu wa atate wako, umtumikire ndi mtima wangwiro ndi moyo waufulu; pakuti Yehova asanthula mitima yonse, nazindikira zolingirira zonse za maganizo; ukamfunafuna Iye udzampeza, koma ukamsiya Iye adzakusiya kosatha.


Yehova Ambuye, ndinu mphamvu ya chipulumutso changa, munandiphimba mutu wanga tsiku lakulimbana nkhondo.


Yehova ndiye mphamvu yanga, ndi chikopa changa; mtima wanga wakhulupirira Iye, ndipo anandithandiza, chifukwa chake mtima wanga ukondwera kwakukulu; ndipo ndidzamyamika nayo nyimbo yanga.


Mundionjole mu ukonde umene ananditchera mobisika. Pakuti Inu ndinu mphamvu yanga.


Adani anga andinyoza ndi kundithyola mafupa anga; pakunena ndine dzuwa lonse, Mulungu wako ali kuti?


Ndidzati kwa Mulungu, thanthwe langa, mwandiiwala chifukwa ninji? Ndimayenderanji wakulira chifukwa cha kundipsinja mdaniyo?


Koma mwatitaya, ndi kutinyazitsa; ndipo simutuluka nao makamu a nkhondo athu.


Musanditaye mu ukalamba wanga; musandisiye, pakutha mphamvu yanga.


Kodi Ambuye adzataya nthawi yonse? Osabwerezanso kukondwera nafe.


Wozunzika ine ndi wofuna kufa kuyambira ubwana wanga; posenza zoopsa zanu, ndithedwa nzeru.


Pakuti Yehova sadzasiya anthu ake, ndipo sadzataya cholowa chake.


Yehova ndiye mphamvu yanga ndi nyimbo yanga, ndipo wakhala chipulumutso changa; ameneyo ndiye Mulungu wanga, ndidzamlemekeza; ndiye Mulungu wa kholo langa, ndidzamveketsa.


koma iwo amene alindira Yehova adzatenganso mphamvu; adzauluka pamwamba ndi mapiko monga ziombankhanga; adzathamanga koma osalema; adzayenda koma osalefuka.


Koma mwa Yehova yekha, wina adzati kwa Ine, muli chilungamo ndi mphamvu; ngakhale kwa Iyeyo anthu adzafika, ndi onse amene anamkwiyira, adzakhala ndi manyazi.


Ndipo ndidzawalimbitsa mwa Yehova; ndipo adzayendayenda m'dzina lake; ati Yehova.


Chotsalira, tadzilimbikani mwa Ambuye, ndi m'kulimba kwa mphamvu yake.


Ndikhoza zonse mwa Iye wondipatsa mphamvuyo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa