Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yakobo 4:9 - Buku Lopatulika

9 Khalani osautsidwa, lirani, lirani misozi; kuseka kwanu kusanduke kulira, ndi chimwemwe chanu chisanduke chisoni.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

9 Khalani osautsidwa, lirani, lirani misozi; kuseka kwanu kusanduke kulira, ndi chimwemwe chanu chisanduke chisoni.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

9 Zindikirani umphaŵi wanu, imvani chisoni, lirani misozi. Kuseka kwanu kusanduke kulira, ndipo chimwemwe chanu chisanduke chisoni.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

9 Chitani chisoni chifukwa cha zimene mwachita, lirani misozi. Kuseka kwanu kusanduke kulira, ndipo chimwemwe chanu chisanduke chisoni.

Onani mutuwo Koperani




Yakobo 4:9
25 Mawu Ofanana  

Ndipo Nehemiya, ndiye kazembe, ndi Ezara wansembe mlembiyo, ndi Alevi ophunzitsa anthu, ananena ndi anthu onse, Lero ndilo lopatulikira Yehova Mulungu wanu, musamachita maliro, musamalira misozi. Popeza anthu onse analira misozi pakumva mau a chilamulo.


Chifukwa chake zeze wanga wasandulika wa maliro, ndi chitoliro changa cha mau a olira misozi.


Maso anga atsitsa mitsinje ya madzi, popeza sasamalira chilamulo chanu.


Ndisanazunzidwe ndinasokera; koma tsopano ndisamalira mau anu.


Kundikomera kuti ndinazunzidwa; kuti ndiphunzire malemba anu.


Ngakhale m'kuseka mtima uwawa; ndipo matsiriziro a chiphwete ndi chisoni.


Ndinati, Kuseka ndi masala; ndi chimwemwe kodi chichita chiyani?


Ndipo namwali adzasangalala m'masewero, ndi anyamata ndi nkhalamba pamodzi; pakuti ndidzasandutsa kulira kwao kukhale kukondwera, ndipo ndidzatonthoza mitima yao, ndi kuwasangalatsa iwo asiye chisoni chao.


Adzadza ndi kulira, ndipo ndidzawatsogolera ndi mapembedzero, ndidzawayendetsa kumitsinje yamadzi, m'njira yoongoka m'mene sadzaphunthwa, pakuti ndili Atate wake wa Israele, ndipo Efuremu ali mwana wanga woyamba.


Chimwemwe cha mtima wathu chalekeka, masewera athu asanduka maliro.


kuti uzikumbukira ndi kuchita manyazi ndi kusatsegulanso pakamwa pako konse, chifukwa chamanyazi ako, pamene ndikufafanizira zonse unazichita, ati Ambuye Yehova.


Ndipo akupulumuka mwa iwo adzapulumuka, koma adzakhala kumapiri ngati njiwa za kuzigwa, onse akubuula, aliyense m'mphulupulu zake.


Iwo ananena kwa Iye, Adzaononga koipa oipawo, nadzapereka mundawo kwa olima ena, amene adzambwezera iye zipatso pa nyengo zake.


Odala ali achisoni; chifukwa adzasangalatsidwa.


Koma Abrahamu anati, Mwana, kumbukira kuti unalandira zokoma zako pakukhala m'moyo iwe, momwemonso Lazaro zoipa; ndipo tsopano iye asangalatsidwa pano, koma iwe uzunzidwadi.


Odala inu akumva njala tsopano; chifukwa mudzakhuta. Odala inu akulira tsopano; chifukwa mudzaseka.


Tsoka inu okhuta tsopano! Chifukwa mudzamva njala. Tsoka inu, akuseka tsopano! Chifukwa mudzachita maliro ndi kulira misozi.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa