Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Amosi 2:2 - Buku Lopatulika

koma ndidzatumiza moto pa Mowabu, udzanyeketsa nyumba zachifumu za Keriyoti; ndipo Mowabu adzafa ndi phokoso, ndi kufuula, ndi mau a lipenga;

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

koma ndidzatumiza moto pa Mowabu, udzanyeketsa nyumba zachifumu za Keriyoti; ndipo Mowabu adzafa ndi phokoso, ndi kufuula, ndi mau a lipenga;

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Nchifukwa chake Ineyo ndidzaponya moto ku Mowabu, ndipo motowo udzapsereza malinga a ku Keriyoti. Anthu a ku Mowabu adzafera pakati pa phokoso la nkhondo, asilikali akufuula ndi kuliza malipenga.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Ine ndidzatumiza moto pa Mowabu, umene udzanyeketsa nyumba zaufumu za ku Keriyoti. Mowabu adzafera pakati pa nkhondo yoopsa, mʼkati mwa mfuwu wa nkhondo ndi kuliza malipenga.

Onani mutuwo



Amosi 2:2
8 Mawu Ofanana  

Pakuti zida zonse za mwamuna wovala zida za nkhondo m'phokosomo, ndi zovala zomvimvinika m'mwazi, zidzakhala zonyeka ngati nkhuni.


ndi pa Keriyoti, ndi pa Bozira, ndi pa mizinda yonse ya dziko la Mowabu, yakutali kapena yakufupi.


Kuyambira kufuula kwa Hesiboni mpaka ku Eleyale, mpaka ku Yahazi anakweza mau, kuyambira pa Zowari mpaka ku Horonaimu, ku Egilati-Selisiya; pakuti pamadzi a ku Nimurimu komwe padzakhala mabwinja.


Keriyoti walandidwa, ndi malinga agwidwa, ndipo tsiku lomwelo mtima wa anthu amphamvu a Mowabu adzakhala ngati mtima wa mkazi alinkudwala.


Iwo amene anathawa aima opanda mphamvu pansi pamthunzi wa Hesiboni; pakuti moto watuluka mu Hesiboni, ndi malawi a moto m'kati mwa Sihoni, nadya ngodya ya Mowabu, ndi pakati pamutu pa ana a phokoso.


Atero Ambuye Yehova, Popeza Mowabu ndi Seiri akuti, Taona nyumba ya Yuda ikunga amitundu onse;


koma ndidzayatsa moto pa linga la Raba, udzanyeketsa nyumba zachifumu zake, ndi kufuula tsiku la nkhondo, ndi namondwe, tsiku la kamvulumvulu;


koma ndidzatumiza moto kunyumba ya Hazaele, ndipo udzanyeketsa nyumba zachifumu za Benihadadi.