Ndipo Yeremiya anati kwa Seraya, Pamene ufika ku Babiloni, samalira kuti uwerenge mau awa onse,
Akolose 4:16 - Buku Lopatulika Ndipo pamene mudamwerenga kalata iyi, amwerengenso mu Mpingo wa ku Laodikea, ndi inunso muwerenge wa ku Laodikea. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo pamene mudamwerenga kalata uyu, amwerengenso mu Mpingo wa ku Laodikea, ndi inunso muwerenge wa ku Laodikea. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Kalatayi itaŵerengedwa pakati panu, ikaŵerengedwenso mu mpingo wa ku Laodikea. Ndipo inunso muŵerengeko kalata imene a ku Laodikea adzakutumizirani. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Kalata iyi ikawerengedwa pakati panu, muonetsetse kuti ikawerengedwenso ku mpingo wa ku Laodikaya ndipo inunso muwerenge kalata yochokera ku Laodikaya. |
Ndipo Yeremiya anati kwa Seraya, Pamene ufika ku Babiloni, samalira kuti uwerenge mau awa onse,
Pakuti ndifuna kuti inu mudziwe nkhawa imene ndili nayo chifukwa cha inu, ndi iwowa a mu Laodikea, ndi onse amene sanaone nkhope yanga m'thupi;
Pakuti ndimchitira iye umboni kuti adziwawitsa nayo ntchito chifukwa cha inu, ndi iwo a mu Laodikea, ndi iwo a mu Hierapoli.
Koma ngati wina samvera mau athu m'kalata iyi, yang'anirani ameneyo, kuti musayanjane naye, kuti achite manyazi.