koma anawatsanzika, nati, Akafuna Mulungu, ndidzabwera kwa inu; ndipo anachoka ku Efeso m'ngalawa.
Ahebri 6:3 - Buku Lopatulika Ndipo ichi tidzachita, akatilola Mulungu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo ichi tidzachita, akatilola Mulungu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mulungu akalola, tidzaterodi. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndipo Mulungu akalola, tidzaterodi. |
koma anawatsanzika, nati, Akafuna Mulungu, ndidzabwera kwa inu; ndipo anachoka ku Efeso m'ngalawa.
kuti ndi chimwemwe ndikadze kwa inu mwa chifuniro cha Mulungu, ndi kupumula pamodzi ndi inu.
Pakuti sindifuna kukuonani tsopano popitirira; pakuti ndiyembekeza kukhala ndi inu nthawi, ngati alola Ambuye.
Koma ndidzafika kwa inu msanga, akandilola Ambuye; ndipo ndidzazindikira si mau a iwo odzitukumula, koma mphamvuyi.
Pakuti sikutheka kuwakonzanso, atembenuke mtima, iwo amene anaunikidwa pa nthawi yake, nalawa mphatso ya Kumwamba, nakhala olandirana naye Mzimu Woyera,