Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




1 Akorinto 4:19 - Buku Lopatulika

19 Koma ndidzafika kwa inu msanga, akandilola Ambuye; ndipo ndidzazindikira si mau a iwo odzitukumula, koma mphamvuyi.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

19 Koma ndidzafika kwa inu msanga, akandilola Ambuye; ndipo ndidzazindikira si mau a iwo odzitukumula, koma mphamvuyi.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

19 Koma Ambuye akalola, ndidzabwera kwanuko posachedwa. Pamenepo ndidzadziŵa zimene odzitukumulawo angathe kuchita, osati zimene amangonena chabe.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

19 Koma ndibwera kwanuko posachedwapa, ngati Ambuye alola, ndipo ndi pamene ndidzadziwe osati zimene anthu odzitukumulawa akuyankhula, koma kuti mphamvu zawo nʼzotani.

Onani mutuwo Koperani




1 Akorinto 4:19
18 Mawu Ofanana  

koma anawatsanzika, nati, Akafuna Mulungu, ndidzabwera kwa inu; ndipo anachoka ku Efeso m'ngalawa.


Ndipo zitatha izi, Paulo anatsimikiza mu mzimu wake, atapita pa Masedoniya ndi Akaya, kunka ku Yerusalemu, kuti, Nditamuka komweko ndiyenera kuonanso ku Roma.


Ndipo m'mene atapitapita m'mbali zijazo, nawachenjeza, anadza ku Grisi.


kuti ndi chimwemwe ndikadze kwa inu mwa chifuniro cha Mulungu, ndi kupumula pamodzi ndi inu.


Ngati wina ali ndi njala adye kwao; kuti mungasonkhanire kwa chiweruziro. Koma zotsalazo ndidzafotokoza pakudza ine.


Ndipo ndifuna inu nonse mulankhule malilime, koma makamaka kuti mukanenere; ndipo wakunenera aposa wakulankhula malilime, akapanda kumasulira, kuti Mpingo ukalandire chomangirira.


Koma ndidzadza kwa inu, nditapyola Masedoniya; pakuti ndidzapyola Masedoniya;


Pakuti sindifuna kukuonani tsopano popitirira; pakuti ndiyembekeza kukhala ndi inu nthawi, ngati alola Ambuye.


Koma tilankhula nzeru mwa angwiro; koma si nzeru ya nthawi ino ya pansi pano, kapena ya akulu a nthawi ino ya pansi pano, amene alinkuthedwa;


Koma ena adzitukumula, monga ngati sindinalinkudza kwa inu.


Koma izi, abale, ndadziphiphiritsira ndekha ndi Apolo, chifukwa cha inu, kuti mwa ife mukaphunzire kusapitirira zimene zilembedwa; kuti pasakhale mmodzi wodzitukumulira mnzake ndi kukana wina.


Koma ine ndiitana Mulungu akhale mboni pa moyo wanga, kuti kulekera inu ndinaleka kudza ku Korinto.


kuti ndisaoneke monga ngati kukuopsani mwa makalatawo.


Ndipo ichi tidzachita, akatilola Mulungu.


Mukadanena inu, Akalola Ambuye, ndipo tikakhala ndi moyo, tidzachita kakutikakuti.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa