Kwa ife ai, Yehova, kwa ife ai, koma kwa dzina lanu patsani ulemerero, chifukwa cha chifundo chanu, ndi choonadi chanu.
Afilipi 4:20 - Buku Lopatulika Ndipo kwa Mulungu ndi Atate wathu kukhale ulemerero kunthawi za nthawi, Amen. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo kwa Mulungu ndi Atate wathu kukhale ulemerero kunthawi za nthawi, Amen. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mulungu Atate athu alemekezedwe mpaka muyaya. Amen. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Kwa Mulungu ndi Atate athu, kukhale ulemerero mpaka muyaya. Ameni. |
Kwa ife ai, Yehova, kwa ife ai, koma kwa dzina lanu patsani ulemerero, chifukwa cha chifundo chanu, ndi choonadi chanu.
Ndipo dzina lake la ulemerero lidalitsike kosatha; ndipo dziko lonse lapansi lidzale nao ulemerero wake. Amen, ndi Amen.
ndi kuwaphunzitsa, asunge zinthu zonse zimene ndinakulamulani inu; ndipo onani, Ine ndili pamodzi ndi inu masiku onse, kufikira chimaliziro cha nthawi ya pansi pano.
Chifukwa chake pempherani inu chomwechi: Atate wathu wa Kumwamba, Dzina lanu liyeretsedwe.
Chifukwa zinthu zonse zichokera kwa Iye, zichitika mwa Iye, ndi kufikira kwa Iye. Kwa Iyeyo ukhale ulemerero kunthawi zonse. Amen.
kwa Mulungu wanzeru yekhayo, mwa Yesu Khristu, kwa yemweyo ukhale ulemerero kunthawi zonse. Amen.
kwa Iye ukhale ulemerero mu Mpingo ndi mwa Khristu Yesu, kufikira mibadwo yonse ya nthawi za nthawi. Amen.
odzala nacho chipatso cha chilungamo, chimene chili mwa Yesu Khristu, kuchitira Mulungu ulemerero ndi chiyamiko.
Ndipo kwa Mfumu yosatha, yosavunda, yosaoneka, Mulungu wa yekha, ukhale ulemu ndi ulemerero, kufikira nthawi za nthawi. Amen.
kwa Mulungu wayekha, Mpulumutsi wathu, mwa Yesu Khristu Ambuye wathu, kukhale ulemerero, ukulu, mphamvu, ndi ulamuliro zisanayambe nthawi, ndi tsopano, ndi kufikira nthawi zonse. Amen.
natiyesa ife ufumu tikhale ansembe a Mulungu ndiye Atate wake; kwa Iye kukhale ulemerero ndi mphamvu kufikira nthawi za nthawi. Amen.
Ndipo panthawipo panali chivomezi chachikulu, ndipo limodzi la magawo khumi a mzinda lidagwa; ndipo anaphedwa m'chivomezicho anthu zikwi zisanu ndi ziwiri; ndipo otsalawo anakhala amantha, napatsa ulemerero kwa Mulungu wa mu Mwamba.
ndi kunena ndi mau aakulu, Opani Mulungu, mpatseni ulemerero; pakuti yafika nthawi ya chiweruziro chake; ndipo mlambireni Iye amene analenga kumwamba ndi dziko lapansi ndi nyanja ndi akasupe amadzi.
akunena ndi mau aakulu, Ayenera Mwanawankhosa, wophedwayo, kulandira chilimbiko, ndi chuma, ndi nzeru, ndi mphamvu, ndi ulemu, ndi ulemerero, ndi chiyamiko.
ndi kunena, Amen: Thamo ndi ulemerero, ndi nzeru, ndi chiyamiko, ndi ulemu, ndi chilimbiko, ndi mphamvu zikhale kwa Mulungu wathu kufikira nthawi za nthawi. Amen.