usaope, pakuti Ine ndili pamodzi ndi iwe; usaopsedwe, pakuti Ine ndine Mulungu wako; ndidzakulimbitsa; inde, ndidzakuthangata; inde, ndidzakuchirikiza ndi dzanja langa lamanja la chilungamo.
Afilipi 4:13 - Buku Lopatulika Ndikhoza zonse mwa Iye wondipatsa mphamvuyo. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndikhoza zonse mwa Iye wondipatsa mphamvuyo. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ndingathe kuchita zonse chifukwa Khristu amandipatsa mphamvu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndikhoza kuchita zonse kudzera mwa Iye amene amandipatsa mphamvu. |
usaope, pakuti Ine ndili pamodzi ndi iwe; usaopsedwe, pakuti Ine ndine Mulungu wako; ndidzakulimbitsa; inde, ndidzakuthangata; inde, ndidzakuchirikiza ndi dzanja langa lamanja la chilungamo.
Koma mwa Yehova yekha, wina adzati kwa Ine, muli chilungamo ndi mphamvu; ngakhale kwa Iyeyo anthu adzafika, ndi onse amene anamkwiyira, adzakhala ndi manyazi.
Ndipo Iye anati, Idza. Ndipo Petro anatsika m'ngalawa, nayenda pamadzi, kufika kwa Yesu.
Ngati mukhala mwa Ine, ndi mau anga akhala mwa inu, pemphani chilichonse chimene muchifuna ndipo chidzachitika kwa inu.
kuti monga mwa chuma cha ulemerero wake akulimbikitseni inu ndi mphamvu mwa Mzimu wake, m'kati mwanu,
olimbikitsidwa m'chilimbiko chonse, monga mwa mphamvu ya ulemerero wake, kuchitira chipiriro chonse ndi kuleza mtima konse pamodzi ndi chimwemwe,
Ndimyamika Iye wondipatsa ine mphamvu, ndiye Khristu Yesu, Ambuye wathu, kuti anandiyesa wokhulupirika, nandiika kuutumiki,