Tapenya wangwiro, ndipo taona woongoka mtima! Pakuti ku matsiriziro ake a munthuyo kuli mtendere.
Afilipi 3:17 - Buku Lopatulika Abale, khalani pamodzi akutsanza anga, ndipo yang'anirani iwo akuyenda kotero monga muli ndi ife chitsanzo chanu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Abale, khalani pamodzi akutsanza anga, ndipo yang'anirani iwo akuyenda kotero monga muli ndi ife chitsanzo chanu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Abale anga, nonse pamodzi muzinditsanzira ine, ndipo muziŵapenyetsetsa amene amayenda motsata chitsanzo chimene ife timakupatsani. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Abale, nonsenu pamodzi mudzinditsanzira ine, ndipo monga inu muli ndi chitsanzo, phunzirani kwa amene akukhala moyo motsatira momwe timakhalira. |
Tapenya wangwiro, ndipo taona woongoka mtima! Pakuti ku matsiriziro ake a munthuyo kuli mtendere.
Ndipo ndikudandaulirani, abale, yang'anirani iwo akuchita zopatutsana ndi zophunthwitsa, kosalingana ndi chiphunzitsocho munachiphunzira inu; ndipo potolokani pa iwo.
Zimenenso mudaziphunzira, ndi kuzilandira, ndi kuzimva, ndi kuziona mwa ine, zomwezo chitani; ndipo Mulungu wa mtendere adzakhala pamodzi ndi inu.
Ndipo munayamba kukhala akutsanza athu, ndi a Ambuye, m'mene mudalandira mauwo m'chisautso chambiri, ndi chimwemwe cha Mzimu Woyera;
Koma ngati wina samvera mau athu m'kalata iyi, yang'anirani ameneyo, kuti musayanjane naye, kuti achite manyazi.
Pakuti mudziwa nokha m'mene muyenera kutitsanza ifemo; pakuti sitinakhale dwakedwake mwa inu;
si chifukwa tilibe ulamuliro, komatu kuti tidzipereke tokha tikhale kwa inu chitsanzo chanu, kuti mukatitsanze ife.
Munthu asapeputse ubwana wako; komatu khala chitsanzo kwa iwo okhulupirira, m'mau, m'mayendedwe, m'chikondi, m'chikhulupiriro, m'kuyera mtima.
Kumbukirani atsogoleri anu, amene analankhula nanu Mau a Mulungu; ndipo poyang'anira chitsiriziro cha mayendedwe ao mutsanze chikhulupiriro chao.