Ndiyo nsembe yopsereza kosalekeza, yoikika kuphiri la Sinai, ichite fungo lokoma, nsembe yamoto ya Yehova.
Afilipi 2:17 - Buku Lopatulika Komatu ngatinso ndithiridwa pa nsembe ndi kutumikira kwa chikhulupiriro chanu, ndikondwera, ndipo ndikondwera pamodzi ndi inu nonse; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Komatu ngatinso ndithiridwa pa nsembe ndi kutumikira kwa chikhulupiriro chanu, ndikondwera, ndipo ndikondwera pamodzi ndi inu nonse; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ndipotu mwina mwake ndidzaphedwa, magazi anga nkukhala ngati otsiridwa pa nsembe imene chikhulupiriro chanu chikupereka kwa Mulungu. Ngati ndi choncho ndili wokondwa, ndipo ndikusangalala nanu pamodzi nonsenu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Koma ngakhale ndikuthiridwa ngati nsembe ya chakumwa yoperekedwa pa nsembe ndi pa utumiki wochokera mʼchikhulupiriro chanu, ndine wokondwa ndi wosangalala pamodzi ndi inu nonse. |
Ndiyo nsembe yopsereza kosalekeza, yoikika kuphiri la Sinai, ichite fungo lokoma, nsembe yamoto ya Yehova.
Ndi nsembe yake yothira ya mwanawankhosa mmodziyo ndiyo limodzi la magawo anai la hini; m'malo opatulika uthirire Yehova nsembe yothira ya chakumwa cholimba.
Komatu sindiuyesa kanthu moyo wanga, kuti uli wa mtengo wake kwa ine ndekha; kotero kuti ndikatsirize njira yanga, ndi utumiki ndinaulandira kwa Ambuye Yesu, kuchitira umboni Uthenga Wabwino wa chisomo cha Mulungu.
Pamenepo Paulo anayankha, Muchitanji, polira ndi kundiswera mtima? Pakuti ndakonzeka ine si kumangidwa kokha, komatunso kufera ku Yerusalemu chifukwa cha dzina la Ambuye Yesu.
Chifukwa chake ndikupemphani inu, abale, mwa zifundo za Mulungu, kuti mupereke matupi anu nsembe yamoyo, yopatulika, yokondweretsa Mulungu, ndiko kupembedza kwanu koyenera.
kuti ndikhale mtumiki wa Khristu Yesu kwa anthu amitundu, wakutumikira Uthenga Wabwino wa Mulungu, kuti kupereka kwake kwa anthu amitundu kulandirike, koyeretsedwa ndi Mzimu Woyera.
Ndipo ndidzapereka ndi kuperekedwa konse chifukwa cha miyoyo yanu mokondweratu. Ngati ndikonda inu kochuluka koposa, kodi ndikondedwa kochepa?
monga akumva chisoni, koma akukondwera nthawi zonse; monga aumphawi, koma akulemeretsa ambiri; monga okhala opanda kanthu, ndipo akhala nazo zinthu zonse.
Ndilimbika mtima kwambiri pakunena nanu, kudzitamandira kwanga chifukwa cha inu nkwakukulu; ndidzazidwa nacho chitonthozo, ndisefukira nacho chimwemwe m'chisautso chathu chonse.
monga mwa kulingiriritsa ndi chiyembekezo changa, kuti palibe chinthu chidzandichititsa manyazi, komatu mwa kulimbika mtima konse, monga nthawi yonse, tsopanonso Khristu adzakuzidwa m'thupi langa, kapena mwa moyo, kapena mwa imfa.
pakuti chifukwa cha ntchito ya Khristu anafikira pafupi imfa, wosasamalira moyo wake, kuti akakwaniritse chiperewero cha utumiki wanu wa kwa ine.
Koma ndili nazo zonse, ndipo ndisefukira; ndadzazidwa, popeza ndalandira kwa Epafrodito zija zidachokera kwanu, mnunkho wa fungo labwino, nsembe yolandirika, yokondweretsa Mulungu.
Tsopano ndikondwera nazo zowawazo chifukwa cha inu, ndipo ndikwaniritsa zoperewera za chisautso cha Khristu m'thupi langa chifukwa cha thupi lake, ndilo Mpingowo;
kotero ife poliralira inu, tinavomera mokondwera kupereka kwa inu si Uthenga Wabwino wa Mulungu wokha, komanso moyo wathu, popeza mudakhala okondedwa kwa ife.
inunso ngati miyala yamoyo mumangidwa nyumba ya uzimu, kuti mukhale ansembe oyera mtima, akupereka nsembe zauzimu, zolandiridwa ndi Mulungu mwa Yesu Khristu.
Umo tizindikira chikondi, popeza Iyeyu anapereka moyo wake chifukwa cha ife; ndipo ife tiyenera kupereka moyo wathu chifukwa cha abale.