3 Yohane 1:2 - Buku Lopatulika Wokondedwa, ndipemphera kuti pa zonse ulemere, nukhale bwino, monga mzimu wako ulemera. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Wokondedwa, ndipemphera kuti pa zonse ulemere, nukhale bwino, monga mzimu wako ulemera. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Wokondedwa, ndimapemphera kuti zako zonse zikuyendere bwino, ndipo kuti moyo wako wathupi ukhale wolimba, monga momwe uliri moyo wako wauzimu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Wokondedwa, ndimakupempherera kuti zako zonse zikuyendere bwino, ndikuti ukhale bwino mʼthupi mwako, monga momwe ulili moyo wako wauzimu. |
Pakutinso anadwaladi pafupi imfa; komatu Mulungu anamchitira chifundo; koma si iye yekha, komatu inenso, kuti ndisakhale nacho chisoni chionjezereonjezere.
Tiziyamika Mulungu nthawi zonse chifukwa cha inu, abale, monga kuyenera; pakuti chikhulupiriro chanu chikula chikulire, ndipo chichulukira chikondano cha inu nonse, yense pa mnzake;
Koma tiyenera ife tiziyamika Mulungu nthawi zonse chifukwa cha inu, abale okondedwa ndi Ambuye, kuti Mulungu anakusankhani inu kuyambira pachiyambi, mulandire chipulumutso mwa chiyeretso cha Mzimu ndi chikhulupiriro cha choonadi;
Koma makamaka, abale anga, musalumbire, kungakhale kutchula kumwamba kapena dziko, kapena lumbiro lina lililonse; koma inde wanu akhale inde, ndi iai wanu akhale iai; kuti mungagwe m'chiweruziro.
koposa zonse mukhale nacho chikondano chenicheni mwa inu nokha; pakuti chikondano chikwiriritsa unyinji wa machimo;
Koma kulani m'chisomo ndi chizindikiritso cha Ambuye wathu ndi Mpulumutsi Yesu Khristu; kwa Iye kukhale ulemerero, tsopano ndi nthawi zonse. Amen.
Ndidziwa chisautso chako, ndi umphawi wako (komatu uli wachuma), ndi mwano wa iwo akunena za iwo okha kuti ali Ayuda, osakhala Ayuda, komatu sunagoge wa Satana.