Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




2 Samueli 8:10 - Buku Lopatulika

Toi anatumiza mwana wake Yoramu kwa mfumu Davide, kuti akamlonjere ndi kumdalitsa, popeza anamenyana ndi Hadadezere ndi kumkantha; pakuti pakati pa Hadadezere ndi Toi panali nkhondo. Ndipo Yoramu anabwera ndi zotengera zasiliva, ndi zotengera zagolide, ndi zotengera zamkuwa.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Toi anatumiza mwana wake Yoramu kwa mfumu Davide, kuti akamlonjere ndi kumdalitsa, popeza anamenyana ndi Hadadezere ndi kumkantha; pakuti pakati pa Hadadezere ndi Toi panali nkhondo. Ndipo Yoramu anabwera ndi zotengera zasiliva, ndi zotengera zagolide, ndi zotengera zamkuwa.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

adatuma mwana wake Yoramu kwa mfumu Davide, kuti akamlonjere. Adaafunanso kukamuyamika chifukwa chakuti adaamenya nkhondo ndi Hadadezere namgonjetsa. Adaatero pakuti Hadadezereyo ankamenyana nkhondo ndi Toi kaŵirikaŵiri. Tsono Yoramuyo adabwera ndi mphatso zopangidwa ndi siliva, golide, ndi mkuŵa.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

anatumiza mwana wake Yoramu kwa mfumu Davide kukamulonjera ndi kukamuyamikira chifukwa cha kupambana kwake pa nkhondo yake ndi Hadadezeriyo, amene analinso pa nkhondo ndi Tou. Yoramu anabweretsa ziwiya zasiliva, zagolide ndi zamkuwa.

Onani mutuwo



2 Samueli 8:10
9 Mawu Ofanana  

Ndipo anafunsa iwo za ubwino wao, nati, Kodi atate wanu ali ndi moyo? Wokalamba uja amene munanena uja: kodi alipo?


Izi zomwe mfumu Davide anazipatula zikhale za Yehova, pamodzi ndi siliva ndi golide anapatulako za amitundu onse adawagonjetsa;


Ndipo pamene Toi mfumu ya ku Hamati anamva kuti Davide adakantha khamu lonse la Hadadezere,


Ndiponso akapolo a mfumu anadzadalitsa Davide mbuye wathu mfumu, nati, Mulungu wanu aposetse dzina la Solomoni lipunde dzina lanu, nakulitse mpando wake wachifumu upose mpando wanu wachifumu; ndipo mfumu anawerama pakamapo.


anatumiza Hadoramu mwana wake kwa mfumu Davide, kumlonjera ndi kumdalitsa, popeza adayambana ndi Hadadezere, namkantha; pakuti Hadadezere adachita nkhondo ndi Tou; ndipo anali nazo zipangizo za mitundumitundu za golide ndi siliva ndi mkuwa.


Ndipo ambiri anabwera nayo mitulo kwa Yehova ku Yerusalemu, ndi za mtengo wake, kwa Hezekiya mfumu ya Yuda; nakwezeka iye pamaso pa amitundu onse kuyambira pomwepo.


Angakhale opitirirapo sanena, Dalitso la Mulungu likhale pa inu; tikudalitsani m'dzina la Yehova.


Nthawi imeneyo Merodaki-Baladani, mwana wa Baladani, mfumu ya ku Babiloni, anatumiza makalata ndi mphatso kwa Hezekiya; pakuti anamva kuti iye anadwala, nachira.


Ndipo kunali kuti pakutsiriza iye kupereka nsembe yopserezayo, pomwepo, onani, Samuele anafika. Ndipo Saulo anamchingamira kukamlonjera iye.