Uriya nanena ndi Davide, Likasalo, ndi Israele, ndi Yuda, alikukhala m'misasa, ndi mbuye wanga Yowabu, ndi anyamata a mbuye wanga alikugona kuthengo, potero ndikapita ine kodi kunyumba yanga kuti ndidye, ndimwe, ndigone ndi mkazi wanga? Pali inu, pali moyo wanu, sindidzachita chinthuchi.