Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Chivumbulutso 2:1 - Buku Lopatulika

1 Kwa mngelo wa Mpingo wa ku Efeso lemba: Izi azinena Iye amene agwira nyenyezi zisanu ndi ziwiri m'dzanja lake lamanja, Iye amene ayenda pakati pa zoikaponyali zisanu ndi ziwiri zagolide:

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

1 Kwa mngelo wa Mpingo wa ku Efeso lemba: Izi azinena Iye amene agwira nyenyezi zisanu ndi ziwiri m'dzanja lake lamanja, Iye amene ayenda pakati pa zoikapo nyali zisanu ndi ziwiri zagolide:

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1 “Mtsogoleri wa mpingo wa ku Efeso umlembere kuti, Naŵa mau ochokera kwa uja wanyamula nyenyezi zisanu ndi ziŵiri m'dzanja lake lamanja, ndi kuyenda pakati pa ndodo za nyale zisanu ndi ziŵiri zagolide zija.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 “Lembera mngelo wa mpingo wa ku Efeso kuti: Awa ndi mawu ochokera kwa amene ali ndi nyenyezi zisanu ndi ziwiri zija mʼdzanja lake lamanja amene akuyenda pakati pa zoyikapo nyale zisanu ndi ziwiri zagolide.

Onani mutuwo Koperani




Chivumbulutso 2:1
20 Mawu Ofanana  

Kalongayo tsono, polowa iwo alowe pakati pao, ndipo potuluka iwo atulukire pamodzi.


Pakuti kumene kuli awiri kapena atatu asonkhanira m'dzina langa, ndili komweko pakati pao.


ndi kuwaphunzitsa, asunge zinthu zonse zimene ndinakulamulani inu; ndipo onani, Ine ndili pamodzi ndi inu masiku onse, kufikira chimaliziro cha nthawi ya pansi pano.


Iyeyo anali nyali yoyaka ndi yowala; ndipo inu munafuna kukondwera m'kuunika kwake kanthawi.


Ndipo iwo anafika ku Efeso, ndipo iye analekana nao pamenepo: koma iye yekha analowa m'sunagoge, natsutsana ndi Ayuda.


koma anawatsanzika, nati, Akafuna Mulungu, ndidzabwera kwa inu; ndipo anachoka ku Efeso m'ngalawa.


Ndipo panali, pamene Apolo anali ku Korinto, Paulo anapita pa maiko a pamtunda, nafika ku Efeso, napeza ophunzira ena;


Ndipo chiphatikizo chake nchanji ndi Kachisi wa Mulungu ndi wa mafano? Pakuti ife ndife Kachisi wa Mulungu wamoyo; monga Mulungu anati, Ndidzakhalitsa mwa iwo, ndipo ndidzayendayenda mwa iwo; ndipo ndidzakhala Mulungu wao, ndi iwo adzakhala anthu anga.


Ndipo m'dzanja lake lamanja munali nyenyezi zisanu ndi ziwiri; ndi m'kamwa mwake mudatuluka lupanga lakuthwa konsekonse; ndipo nkhope yake ngati dzuwa lowala mu mphamvu yake.


chinsinsi cha nyenyezi zisanu ndi ziwiri zimene unaziona padzanja langa lamanja, ndi zoikaponyali zisanu ndi ziwiri zagolide: nyenyezi zisanu ndi ziwiri ndizo angelo a Mipingo isanu ndi iwiri; ndipo zoikaponyali zisanu ndi ziwiri ndizo Mipingo isanu ndi iwiri.


Ndipo chizindikiro chachikulu chinaoneka m'mwamba; mkazi wovekedwa dzuwa, ndi mwezi kumapazi ake, ndi pamutu pake korona wa nyenyezi khumi ndi ziwiri;


Ndipo kwa mngelo wa Mpingo wa ku Pergamo lemba: Izi anena Iye wokhala nalo lupanga lakuthwa konsekonse:


Ndipo kwa mngelo wa Mpingo wa ku Tiatira lemba: Izi azinena Mwana wa Mulungu, wakukhala nao maso ake ngati lawi la moto, ndi mapazi ake ngati mkuwa wonyezimira:


Ndipo kwa mngelo wa Mpingo wa ku Smirina lemba: Izi anena woyamba ndi wotsiriza, amene anakhala wakufa, nakhalanso ndi moyo:


Ndipo kwa mngelo wa Mpingo wa ku Sardi lemba: Izi anena Iye wakukhala nayo mizimu isanu ndi iwiri ya Mulungu, ndi nyenyezi zisanu ndi ziwiri: Ndidziwa ntchito zako, kuti uli nalo dzina lakuti uli ndi moyo, ndipo uli wakufa.


Ndipo kwa mngelo wa Mpingo wa ku Laodikea lemba: Izi anena Ameni'yo, mboni yokhulupirika ndi yoona, woyamba wa chilengo cha Mulungu:


Ndipo kwa mngelo wa Mpingo wa ku Filadelfiya lemba: Izi anena Iye amene ali Woyera, Iye amene ali Woona, Iye wakukhala nacho chifungulo cha Davide, Iye wotsegula, ndipo palibe wina atseka; Iye wotseka, ndipo palibe wina atsegula:


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa