6 Pakuti sindinakhale m'nyumba kuyambira tsiku lija ndinatulutsa ana a Israele ku Ejipito kufikira lero lomwe, koma ndinayenda m'chihema ndi m'nyumba wamba.
6 Pakuti sindinakhala m'nyumba kuyambira tsiku lija ndinatulutsa ana a Israele ku Ejipito kufikira lero lomwe, koma ndinayenda m'chihema ndi m'nyumba wamba.
Uriya anayankha Davide kuti, “Bokosi la Chipangano ndi Israeli ndiponso Yuda akukhala mʼmatenti, ndipo mbuye wanga Yowabu ndi ankhondo anu mbuye wanga amanga misasa pa mtetete. Ine ndingapite bwanji ku nyumba yanga kukadya ndi kumwa ndiponso kugona ndi mkazi wanga? Pali inu wamoyo, ine sindidzachita chinthu chimenechi.”
Pali mgwirizano wanji pakati pa Nyumba ya Mulungu ndi nyumba ya mafano? Popezatu ndife Nyumba ya Mulungu wamoyo. Monga Mulungu wanena kuti, “Ndidzakhala mwa iwo ndipo ndidzayendayenda pakati pawo, ndipo ndidzakhala Mulungu wawo, ndipo adzakhala anthu anga.”
Pakuti Yehova Mulungu wanu amayendayenda ku msasa wanu kukutchinjirizani ndi kupereka adani anu kwa inu. Nʼchifukwa chake msasa wanu uzikhala wopatulika kuti mwina angaone china chonyansa nabwerera osakuyandikirani.
“Lembera mngelo wa mpingo wa ku Efeso kuti: Awa ndi mawu ochokera kwa amene ali ndi nyenyezi zisanu ndi ziwiri zija mʼdzanja lake lamanja amene akuyenda pakati pa zoyikapo nyale zisanu ndi ziwiri zagolide.