2 Samueli 11:11 - Buku Lopatulika11 Uriya nanena ndi Davide, Likasalo, ndi Israele, ndi Yuda, alikukhala m'misasa, ndi mbuye wanga Yowabu, ndi anyamata a mbuye wanga alikugona kuthengo, potero ndikapita ine kodi kunyumba yanga kuti ndidye, ndimwe, ndigone ndi mkazi wanga? Pali inu, pali moyo wanu, sindidzachita chinthuchi. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201411 Uriya nanena ndi Davide, Likasalo, ndi Israele, ndi Yuda, alikukhala m'misasa, ndi mbuye wanga Yowabu, ndi anyamata a mbuye wanga alikugona kuthengo, potero ndikapita ine kodi kunyumba yanga kuti ndidye, ndimwe, ndigone ndi mkazi wanga? Pali inu, pali moyo wanu, sindidzachita chinthuchi. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa11 Uriya adauza Davide kuti, “Bokosi lachipangano likukhala m'zithando, kudzanso Aisraele ndi Ayuda. Ndipo mbuyanga Yowabu pamodzi ndi ankhondo a mfumu akugona panja pamtetete. Ndiye ine ndingapite kunyumba kwanga kuti ndizikadya ndi kumwa, ndi kumakakhala ndi mkazi wanga? Pali inu amene, ine sindingachite zimenezo.” Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero11 Uriya anayankha Davide kuti, “Bokosi la Chipangano ndi Israeli ndiponso Yuda akukhala mʼmatenti, ndipo mbuye wanga Yowabu ndi ankhondo anu mbuye wanga amanga misasa pa mtetete. Ine ndingapite bwanji ku nyumba yanga kukadya ndi kumwa ndiponso kugona ndi mkazi wanga? Pali inu wamoyo, ine sindidzachita chinthu chimenechi.” Onani mutuwo |
Ndipo mfumuyo inati, Kodi Yowabu adziwana ndi iwe mwa izi zonse? Mkaziyo nayankha nati, Pali moyo wanu mbuye wanga mfumu, palibe kulewa ku dzanja lamanja, kapena kulamanzere kwa zonse mudazinena mbuye wanga mfumu; pakuti mnyamata wanu Yowabu ndiye anandiuza, naika mau onse awa m'kamwa mwa mdzakazi wanu.