Pakuti, chifukwa cha kusalinyamula inu poyamba paja, Yehova Mulungu wathu anachita chotipasula, popeza sitinamfunafuna Iye monga mwa chiweruzo.
2 Samueli 6:3 - Buku Lopatulika Ndipo iwo ananyamulira likasa la Mulungu pa galeta watsopano, atalitulutsa m'nyumba ya Abinadabu, ili pachitunda, ndipo Uza ndi Ahiyo ana a Abinadabu anayendetsa ng'ombe za pa galeta watsopanoyo. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo iwo ananyamulira likasa la Mulungu pa galeta watsopano, atalitulutsa m'nyumba ya Abinadabu, ili pachitunda, ndipo Uza ndi Ahiyo ana a Abinadabu anayendetsa ng'ombe za pa galeta watsopanoyo. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Anthuwo adatulutsa Bokosi lachipanganolo m'nyumba ya Abinadabu, imene inali pa phiri, nalinyamula pa ngolo yatsopano. Tsono Uza ndi Ahiyo, ana a Abinadabu, ndiwo ankayendetsa ngolo yatsopanoyo Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Iwo anayika Bokosi la Mulungu pa ngolo yatsopano nachoka nalo ku nyumba ya Abinadabu, imene inali pa phiri. Uza ndi Ahiyo ana a Abinadabu ndiwo ankayendetsa ngolo yatsopanoyo, |
Pakuti, chifukwa cha kusalinyamula inu poyamba paja, Yehova Mulungu wathu anachita chotipasula, popeza sitinamfunafuna Iye monga mwa chiweruzo.
Chifukwa chake tsono, tengani, nimukonze galeta latsopano, ndi ng'ombe ziwiri zamkaka, zosalawa goli chikhalire, ndipo mumange ng'ombezo pagaleta, muzichotsere ana ao kunka nao kwanu;
Ndipo anthu a ku Kiriyati-Yearimu anabwera, natenga likasa la Yehova, nafika nalo m'nyumba ya Abinadabu paphiri; napatula mwana wake wamwamuna Eleazara kuti asunge likasa la Yehova.