Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




1 Samueli 6:7 - Buku Lopatulika

7 Chifukwa chake tsono, tengani, nimukonze galeta latsopano, ndi ng'ombe ziwiri zamkaka, zosalawa goli chikhalire, ndipo mumange ng'ombezo pagaleta, muzichotsere ana ao kunka nao kwanu;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

7 Chifukwa chake tsono, tengani, nimukonze galeta latsopano, ndi ng'ombe ziwiri zamkaka, zosalawa goli chikhalire, ndipo mumange ng'ombezo pagaleta, muzichotsere ana ao kunka nao kwanu;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

7 Ndiye inu, konzani galeta latsopano ndipo mutenge ng'ombe ziŵiri zazikazi zamkaka zimene sizidavalepo goli ndi kale lonse. Mumange ng'ombezo ku galeta, koma makonyani ake muŵasiye kumudzi kwanu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

7 “Tsopano konzani galeta latsopano limodzi ndiponso ngʼombe ziwiri zazikazi zamkaka zimene sizinavalepo goli. Muzimangirire ngʼombezo ku ngoloyo, koma ana awo muwachotse ndi kuwasiya kwanu.

Onani mutuwo Koperani




1 Samueli 6:7
5 Mawu Ofanana  

Ndipo iwo ananyamulira likasa la Mulungu pa galeta watsopano, atalitulutsa m'nyumba ya Abinadabu, ili pachitunda, ndipo Uza ndi Ahiyo ana a Abinadabu anayendetsa ng'ombe za pa galeta watsopanoyo.


Ndipo anatengera likasa la Mulungu pa galeta watsopano kuchokera kunyumba ya Abinadabu; ndi Uza ndi Ahiyo anayendetsa ng'ombe za pa galetayo.


Ili ndi lemba la chilamulo Yehova adalamulirachi, ndi kuti, Nena ndi ana a Israele kuti azikutengera ng'ombe yaikazi yofiira, yangwiro yopanda chilema, yosamanga m'goli;


ndipo kudzali kuti mzinda wakukhala kufupi kwa munthu wophedwayo, inde akulu a mzinda uwu atenge ng'ombe yaikazi yosagwira ntchito, yosakoka goli;


ndipo akulu a mzinda uwu atsike nayo ng'ombeyo ku chigwa choyendako madzi, chosalima ndi chosabzala, nayidula khosi ng'ombeyo m'chigwamo;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa