Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Samueli 6:3 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

3 Iwo anayika Bokosi la Mulungu pa ngolo yatsopano nachoka nalo ku nyumba ya Abinadabu, imene inali pa phiri. Uza ndi Ahiyo ana a Abinadabu ndiwo ankayendetsa ngolo yatsopanoyo,

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

3 Ndipo iwo ananyamulira likasa la Mulungu pa galeta watsopano, atalitulutsa m'nyumba ya Abinadabu, ili pachitunda, ndipo Uza ndi Ahiyo ana a Abinadabu anayendetsa ng'ombe za pa galeta watsopanoyo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

3 Ndipo iwo ananyamulira likasa la Mulungu pa galeta watsopano, atalitulutsa m'nyumba ya Abinadabu, ili pachitunda, ndipo Uza ndi Ahiyo ana a Abinadabu anayendetsa ng'ombe za pa galeta watsopanoyo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

3 Anthuwo adatulutsa Bokosi lachipanganolo m'nyumba ya Abinadabu, imene inali pa phiri, nalinyamula pa ngolo yatsopano. Tsono Uza ndi Ahiyo, ana a Abinadabu, ndiwo ankayendetsa ngolo yatsopanoyo

Onani mutuwo Koperani




2 Samueli 6:3
6 Mawu Ofanana  

Popeza kuti inu Alevi simunalinyamule poyamba paja, Yehova Mulungu wathu anatikantha. Sitinafunse momwe tikanachitira monga mmene Iyeyo anafotokozera.”


Zoonadi, tinamva za Bokosi la Chipangano ku Efurata, tinalipeza mʼminda ya ku Yaara:


“Tsopano konzani galeta latsopano limodzi ndiponso ngʼombe ziwiri zazikazi zamkaka zimene sizinavalepo goli. Muzimangirire ngʼombezo ku ngoloyo, koma ana awo muwachotse ndi kuwasiya kwanu.


Choncho anthu a ku Kiriati-Yearimu anabwera ndi kudzatenga Bokosi la Yehova. Iwo anapita nalo ku nyumba ya Abinadabu ya ku phiri ndipo anapatula Eliezara mwana wake kuti aziyangʼanira Bokosi la Yehovalo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa