Pomwepo mfumu inanena kwa Itai Mgiti, Bwanji ulikupita nafe iwenso? Ubwerere nukhale ndi mfumu; pakuti uli mlendo ndi wopirikitsidwa; bwerera ku malo a iwe wekha.
2 Samueli 6:10 - Buku Lopatulika Momwemo Davide sanafune kudzitengera likasa la Yehova lidze kumzinda wa Davide; koma Davide analipambutsira kunyumba ya Obededomu Mgiti. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Momwemo Davide sanafune kudzitengera likasa la Yehova lidze kumudzi wa Davide; koma Davide analipambutsira kunyumba ya Obededomu Mgiti. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Motero Davide sadafunenso kuti abwere nalo Bokosi la Chautalo kwao ku mzinda wake wa Davide, koma adalipatutsira ku nyumba ya Obededomu Mgiti. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Iye sanafunenso kubwera ndi Bokosi la Yehova kawo ku mzinda wake wa Davide. Mʼmalo mwake anapita nalo ku nyumba ya Obedi-Edomu Mgiti. |
Pomwepo mfumu inanena kwa Itai Mgiti, Bwanji ulikupita nafe iwenso? Ubwerere nukhale ndi mfumu; pakuti uli mlendo ndi wopirikitsidwa; bwerera ku malo a iwe wekha.
Davide natumiza anthu atawagawa magulu atatu, gulu limodzi aliyang'anire Yowabu, lina aliyang'anire Abisai, mwana wa Zeruya, mbale wa Yowabu, ndi lina aliyang'anire Itai Mgiti. Ndipo mfumu inanena ndi anthu, Zoonadi ine ndemwe ndidzatuluka limodzi ndi inu.
Ndipo Davide anakhala m'linga muja, nalitcha mzinda wa Davide. Davide namanga linga pozinga ponse kuyambira ku Milo ndi m'kati momwe.
ndi pamodzi nao abale ao a kulongosola kwachiwiri, Zekariya, Beni, ndi Yaaziele, ndi Semiramoti, ndi Yehiyele, ndi Uni, Eliyabu, ndi Benaya, ndi Maaseiya, ndi Matitiya, ndi Elifelehu, ndi Mikineya, ndi Obededomu, ndi Yeiyele, odikirawo.
Ndi Sebaniya, ndi Yosafati, ndi Netanele, ndi Amasai, ndi Zekariya, ndi Benaya, ndi Eliyezere, ansembe, analiza malipenga ku likasa la Mulungu; ndi Obededomu ndi Yehiya anali odikira a likasa.
Asafu ndiye mkulu wao, ndi otsatana naye Zekariya, Yeiyele, ndi Semiramoti, ndi Yehiyele, ndi Matitiya, ndi Eliyabu, ndi Benaya, ndi Obededomu, ndi Yeiyele, ndi zisakasa ndi azeze; koma Asafu ndi nsanje zomvekatu;