Ndipo m'tsogolo mwake Davide anakantha Afilisti, nawagonjetsa Davide nalanda mudzi wa Metege Ama m'manja mwa Afilisti.
2 Samueli 5:25 - Buku Lopatulika Ndipo Davide anatero, monga Yehova anamlamulira, nakantha Afilisti kuyambira ku Geba kufikira ku Gezere. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Davide anatero, monga Yehova anamlamulira, nakantha Afilisti kuyambira ku Geba kufikira ku Gezere. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Davide adachitadi monga momwe Chauta adaamlamulira, ndipo adagonjetsa Afilistiwo kuyambira ku Geba mpaka ku Gezere. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Kotero Davide anachita zimene Yehova anamulamulira ndipo anakantha Afilisti njira yonse kuchokera ku Geba mpaka ku Gezeri. |
Ndipo m'tsogolo mwake Davide anakantha Afilisti, nawagonjetsa Davide nalanda mudzi wa Metege Ama m'manja mwa Afilisti.
Nachita Davide monga Mulungu adamuuza, nakantha gulu la Afilisti kuyambira ku Gibiyoni kufikira ku Gezere.
Ndipo anthu anawerama, nalambira. Ndipo ana a Israele anamuka nachita monga Yehova adalamulira Mose ndi Aroni; anachita momwemo.
Pakuti Yehova adzauka monga m'phiri la Perazimu, nadzakwiya monga m'chigwa cha Gibiyoni; kuti agwire ntchito yake, ntchito yake yachilendo, ndi kuti achite chochita chake, chochita chake chachilendo.
Pamenepo Horamu mfumu ya Gezere anakwera kudzathandiza Lakisi; ndipo Yoswa anamkantha iye ndi anthu ake mpaka sanamsiyire ndi mmodzi yense.
Ndipo sanaingitse Akanani akukhala mu Gezere; koma Akanani anakhala pakati pa Efuremu, kufikira lero lino, nawaumiriza kugwira ntchito yathangata.
Ndipo anawapatsa Sekemu ndi mabusa ake ku mapiri a Efuremu, ndiwo mzinda wopulumukirako wakupha mnzakeyo, ndi Gezere ndi mabusa ake;