Ndipo Afilisti anaponyananso nkhondo ndi Aisraele; ndipo Davide anatsika ndi anyamata ake pamodzi naye naponyana ndi Afilisti; nafuna kukomoka Davide.
2 Samueli 5:17 - Buku Lopatulika Koma pamene Afilisti anamva kuti adamdzoza Davide mfumu ya Israele, Afilisti onse anakwera kukafuna Davide; ndipo Davide anachimva natsikira kungaka kuja. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Koma pamene Afilisti anamva kuti adamdzoza Davide mfumu ya Israele, Afilisti onse anakwera kukafuna Davide; ndipo Davide anachimva natsikira kungaka kuja. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Afilisti atamva kuti Davide wadzozedwa kukhala mfumu yolamulira dziko la Aisraele, adapita kukamfunafuna. Koma Davide atamva zimenezo, adatsikira ku linga. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Afilisti atamva kuti Davide wadzozedwa kukhala mfumu ya Israeli, iwo anapita mwamphamvu kukamusakasaka. Koma Davide atamva zimenezi anakalowa mu linga. |
Ndipo Afilisti anaponyananso nkhondo ndi Aisraele; ndipo Davide anatsika ndi anyamata ake pamodzi naye naponyana ndi Afilisti; nafuna kukomoka Davide.
Ndipo m'tsogolo mwake Davide anakantha Afilisti, nawagonjetsa Davide nalanda mudzi wa Metege Ama m'manja mwa Afilisti.
za Aaramu, za Amowabu, za ana a Amoni, za Afilisti, za Amaleke, ndi zofunkha za Hadadezere, mwana wa Rehobu mfumu ya ku Zoba.
amene mwa chikhulupiriro anagonjetsa maufumu, anachita chilungamo, analandira malonjezano, anatseka pakamwa pa mikango,
Tsono Afilisti anasonkhanitsa makamu ao onse ku Afeki; ndipo Aisraele anamanga ku chitsime cha mu Yezireele.