Koma mau a mfumu anapambana Yowabu ndi atsogoleri a khamulo. Ndipo Yowabu ndi atsogoleri a khamulo anatuluka pamaso pa mfumu kuti akawerenge anthu a Israele.
2 Samueli 24:5 - Buku Lopatulika Naoloka Yordani, namanga zithando ku Aroere ku dzanja lamanja kwa mzinda uli pakati pa chigwa cha Gadi, ndi ku Yazere; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Naoloka Yordani, namanga zithando ku Aroere ku dzanja lamanja kwa mudzi uli pakati pa chigwa cha Gadi, ndi ku Yazere; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Adaoloka mtsinje wa Yordani, nayambira ku Aroere, mzinda umene uli pakati pa chigwa cha ku Gadi, mpaka ku Yazere. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Atawoloka Yorodani, iwo anamanga misasa yawo pafupi ndi Aroeri kummwera kwa mzinda wa ku chigwa ndipo kenaka iwo anapita ku dziko la Gadi mpaka ku Yazeri. |
Koma mau a mfumu anapambana Yowabu ndi atsogoleri a khamulo. Ndipo Yowabu ndi atsogoleri a khamulo anatuluka pamaso pa mfumu kuti akawerenge anthu a Israele.
Ndipo Mose anatumiza anthu akazonde Yazere, nalanda midzi yake, napirikitsa Aamori a komweko.
Koma ana a Rubeni ndi ana Gadi anali nazo zoweta zambirimbiri; ndipo anapenyerera dziko la Yazere, ndi dziko la Giliyadi, ndipo taonani, malowo ndiwo malo a zoweta.
Ataroti, ndi Diboni, ndi Yazere, ndi Nimira, ndi Hesiboni, ndi Eleyale, ndi Sibima, ndi Nebo, ndi Beoni,
Kuyambira ku Aroere, ndiko kumphepete kwa mtsinje wa Arinoni, ndi kumudzi wokhala kumtsinje kufikira ku Giliyadi, kunalibe mzinda wakutitalikira malinga ake; Yehova Mulungu wathu anapereka yonse pamaso pathu.
Malire ao anayambira ku Aroere wokhala m'mphepete mwa chigwa cha Arinoni, ndi mzinda uli pakati pa chigwa ndi chidikha chonse cha ku Medeba;
Ndipo malire ao ndiwo Yazere, ndi mizinda yonse ya Giliyadi, ndi dziko la ana a Amoni logawika pakati, mpaka ku Aroere, wokhala chakuno cha Raba;
kuyambira pa Aroere, wokhala m'mphepete mwa chigwa cha Arinoni, ndi mzinda uli pakati pa chigwa, ndi chidikha chonse cha Medeba mpaka ku Diboni;