Yoswa 13:9 - Buku Lopatulika9 kuyambira pa Aroere, wokhala m'mphepete mwa chigwa cha Arinoni, ndi mzinda uli pakati pa chigwa, ndi chidikha chonse cha Medeba mpaka ku Diboni; Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20149 kuyambira pa Aroere, wokhala m'mphepete mwa chigwa cha Arinoni, ndi mudzi uli pakati pa chigwa, ndi chidikha chonse cha Medeba mpaka ku Diboni; Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa9 Dziko laolo lidayambira ku Aroere, mzinda umene uli pafupi ndi chigwa cha Arinoni, ndiponso ku mzinda wokhala pakati pa chigwacho. Dzikolo linkaphatikiza dera lonse lokwera kuyambira ku Medeba kukafika ku Diboni. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero9 Dziko lawolo linayambira ku Aroeri mzinda umene uli pafupi ndi chigwa cha Arinoni, ndiponso mzinda umene uli pakati pa chigwacho. Dzikolo linkaphatikizanso dera lonse lokwera kuyambira ku Medeba mpaka ku Diboni. Onani mutuwo |