Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




2 Samueli 23:22 - Buku Lopatulika

Izi anachita Benaya mwana wa Yehoyada, natenga dzina mwa ngwazi zitatuzo.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Izi anachita Benaya mwana wa Yehoyada, natenga dzina mwa ngwazi zitatuzo.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Zimenezi ndi ntchito zimene adatchuka nazo Benaya mwana wa Yehoyada, yemwe anali m'modzi wa anthu makumi atatu amphamvu aja.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Izi ndi zamphamvu zimene Benaya mwana wa Yehoyada anachita. Iyeyo analinso wotchuka ngati anthu atatu amphamvu aja.

Onani mutuwo



2 Samueli 23:22
5 Mawu Ofanana  

Ndipo anatuluka namtsata anthu a Yowabu, ndi Akereti ndi Apeleti, ndi anthu onse amphamvu; natuluka mu Yerusalemu kukalondola Sheba mwana wa Bikiri.


Ndipo Benaya, mwana wa Yehoyada, mwana wa ngwazi wa ku Kabizeeli amene anachita zamphamvu; iye anapha anthu awiri a Mowabu akunga mikango, natsikanso iye napha mkango m'mbuna nyengo ya chipale chofewa;


ndipo anapha Mwejipito munthu wokongola, Mwejipito anali nao mkondo m'dzanja lake; koma iyeyo anatsikira kwa iye ndi ndodo, nasolola mkondowo m'dzanja la Mwejipito, namupha ndi mkondo wa iye mwini.


Iye ndiye waulemu koposa makumi atatuwo, koma sadafikane ndi atatu oyamba. Ndipo Davide anamuika kuyang'anira olindirira ake.


Ndipo Benaya mwana wa Yehoyada anayang'anira Akereti ndi Apeleti. Ndipo ana a Davide anali ansembe ake.