Ndipo Yakobo anaimiritsa mwala pamalo pamene ananena ndi iye, choimiritsa chamwala: ndipo anathira pamenepo nsembe yothira, nathirapo mafuta.
2 Samueli 23:16 - Buku Lopatulika Ndipo ngwazi zitatuzo zinapyola khamu la Afilisti, ndipo zinatunga madzi m'chitsime cha ku Betelehemu, cha pa chipatacho, nawatenga, nafika nao kwa Davide; koma iye sanafune kumwako, koma anawathira pansi kwa Yehova. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo ngwazi zitatuzo zinapyola khamu la Afilisti, nizitunga madzi m'chitsime cha ku Betelehemu, cha pa chipatacho, nawatenga, nafika nao kwa Davide; koma iye sanafune kumwako, koma anawathira pansi kwa Yehova. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pamenepo anthu atatu amphamvu aja adapita, nabzola zithando za Afilisti, nkutunga madzi m'chitsime cha ku Betelehemu, chimene chinali pafupi ndi chipata. Adatenga madziwo, nabwera nawo kwa Davide. Koma Davideyo sadafune kumwako madziwo adangoŵathira pansi, kuŵapereka kwa Chauta, Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Choncho anthu amphamvu atatuwa anadutsa mizere ya Afilisti, natunga madzi amene anali mʼchitsime chomwe chinali pafupi ndi chipata cha ku Betelehemu nabwera nawo kwa Davide. Koma iye anakana kumwa. Mʼmalo mwake anathira pansi pamaso pa Yehova. |
Ndipo Yakobo anaimiritsa mwala pamalo pamene ananena ndi iye, choimiritsa chamwala: ndipo anathira pamenepo nsembe yothira, nathirapo mafuta.
Ndipo wotsatana naye Eleazara mwana wa Dodo mwana wa Mwahohi, mmodzi wa ngwazi zitatu zokhala ndi Davide pamene iwo anatonza Afilisti osonkhanidwa kunkhondo kumeneko, atachoka Aisraele;
Napyola atatuwo misasa ya Afilisti natunga madzi ku chitsime cha ku Betelehemu chili kuchipata, nabwera nao kwa Davide; koma Davide anakana kumwako, koma anawathirira kwa Yehova;
Ndipo wina akamgonjetsa mmodziyo, awiri adzachilimika; ndipo chingwe cha nkhosi zitatu sichiduka msanga.
Tauka, tafuula usiku, poyamba kulonda; tsanulira mtima wako ngati madzi pamaso pa Ambuye; takwezera maso ako kwa Iye, chifukwa cha moyo wa tiana tako, timene tilefuka ndi njala pa malekezero a makwalala onse.
Ndi nsembe yake yothira ya mwanawankhosa mmodziyo ndiyo limodzi la magawo anai la hini; m'malo opatulika uthirire Yehova nsembe yothira ya chakumwa cholimba.
Komatu sindiuyesa kanthu moyo wanga, kuti uli wa mtengo wake kwa ine ndekha; kotero kuti ndikatsirize njira yanga, ndi utumiki ndinaulandira kwa Ambuye Yesu, kuchitira umboni Uthenga Wabwino wa chisomo cha Mulungu.
Pakuti ndi chivuto munthu adzafera wina wolungama; pakuti kapena wina adzalimbika mtima kufera munthu wabwino.
Pakuti chikondi cha Khristu chitikakamiza; popeza taweruza chotero, kuti mmodzi adafera onse, chifukwa chake onse adafa;
Komatu ngatinso ndithiridwa pa nsembe ndi kutumikira kwa chikhulupiriro chanu, ndikondwera, ndipo ndikondwera pamodzi ndi inu nonse;
popeza iye anataya moyo wake nakantha Mfilistiyo, ndipo Yehova anachitira Aisraele onse chipulumutso chachikulu, inu munachiona, nimunakondwera; tsono mudzachimwiranji mwazi wosalakwa, ndi kumupha Davide popanda chifukwa?
Ndipo anaunjikana ku Mizipa, natunga madzi, nawatsanula pamaso pa Yehova, nasala chakudya tsiku lija, nati, Tinachimwira Yehova. Ndipo Samuele anaweruza ana a Israele mu Mizipa.