Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Mlaliki 4:12 - Buku Lopatulika

12 Ndipo wina akamgonjetsa mmodziyo, awiri adzachilimika; ndipo chingwe cha nkhosi zitatu sichiduka msanga.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

12 Ndipo wina akamlaka mmodziyo, awiri adzachilimika; ndipo chingwe cha m'khosi zitatu sichiduka msanga.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

12 Nkotheka kuti munthu apambane mnzake amene ali yekha, koma pakakhala aŵiri, iwoŵa adzalimbana naye. Chingwe cha nkhosi zitatu sichidukirapo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

12 Munthu mmodzi angathe kugonjetsedwa, koma anthu awiri akhoza kudziteteza. Chingwe cha maulusi atatu sichidukirapo.

Onani mutuwo Koperani




Mlaliki 4:12
8 Mawu Ofanana  

Ndipo ngwazi zitatuzo zinapyola khamu la Afilisti, ndipo zinatunga madzi m'chitsime cha ku Betelehemu, cha pa chipatacho, nawatenga, nafika nao kwa Davide; koma iye sanafune kumwako, koma anawathira pansi kwa Yehova.


Iye ndiye waulemu koposa makumi atatuwo, koma sadafikane ndi atatu oyamba. Ndipo Davide anamuika kuyang'anira olindirira ake.


Ndipo wotsatana naye Eleazara mwana wa Dodo mwana wa Mwahohi, mmodzi wa ngwazi zitatu zokhala ndi Davide pamene iwo anatonza Afilisti osonkhanidwa kunkhondo kumeneko, atachoka Aisraele;


Ndiponso awiri akagona limodzi afunditsana; koma mmodzi pa yekha kodi adzafunditsidwa bwanji?


Mnyamata wosauka ndi wanzeru apambana mfumu yokalamba ndi yopusa, imene sifunanso kulangidwa mwambo.


ndi kusamalitsa kusunga umodzi wa Mzimu mwa chimangiriro cha mtendere.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa