Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Mlaliki 4:13 - Buku Lopatulika

13 Mnyamata wosauka ndi wanzeru apambana mfumu yokalamba ndi yopusa, imene sifunanso kulangidwa mwambo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

13 Mnyamata wosauka ndi wanzeru apambana mfumu yokalamba ndi yopusa, imene sifunanso kulangidwa mwambo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

13 Mnyamata wosauka ndi wanzeru ali bwino kupambana mfumu yokalamba ndi yopusa, imene siikumvanso malangizo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

13 Wachinyamata wosauka koma wanzeru aposa mfumu yokalamba koma yopusa imene simvanso malangizo.

Onani mutuwo Koperani




Mlaliki 4:13
11 Mawu Ofanana  

Mibadwo ya Yakobo ndi iyi; Yosefe anali wa zaka khumi ndi zisanu ndi ziwiri analinkudyetsa zoweta pamodzi ndi abale ake; ndipo anali mnyamata pamodzi ndi ana a Biliha, ndi ana aamuna a Zilipa, akazi a atate wake; ndipo Yosefe anamfotokozera atate wake mbiri yao yoipa.


Ndipo mfumu ya Israele inati kwa Yehosafati, Alipo munthu wina kuti tifunsire kwa Yehova mwa iye; koma ndimuda, popeza samanenera za ine zabwino, koma zoipa; ndiye Mikaya mwana wake wa Imila. Nati Yehosafati, Isamatero mfumu.


Ndipo kunali, pakulankhula naye mfumu, inanena naye, Takuika kodi ukhale wopangira mfumu? Leka, angakukanthe. Pamenepo mneneriyo analeka, nati, Ndidziwa kuti Mulungu watsimikiza mtima kukuonongani, popeza mwachita ichi ndi kusamvera kupangira kwanga.


Wosauka woyenda mwangwiro aposa wokhetsa milomo ndi wopusa.


Waumphawi woyenda mwangwiro apambana ndi yemwe akhotetsa njira zake, angakhale alemera.


Ndipo wina akamgonjetsa mmodziyo, awiri adzachilimika; ndipo chingwe cha nkhosi zitatu sichiduka msanga.


Nzeru ilimbitsa wanzeru koposa akulu khumi akulamulira m'mzinda.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa