iye ananyamuka, nakantha Afilisti kufikira dzanja lake linalema, ndi dzanja lake lomamatika kulupanga; ndipo Yehova anachititsa chipulumutso chachikulu tsiku lija, ndipo anthu anabwera m'mbuyo mwake kukafunkha kokha.
2 Samueli 23:12 - Buku Lopatulika Koma iyeyo anaima pakati pamundawo, nautchinjiriza, napha Afilistiwo. Ndipo Yehova anachititsa chipulumutso chachikulu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Koma iyeyo anaima pakati pa mundawo, nautchinjiriza, napha Afilistiwo. Ndipo Yehova anachititsa chipulumutso chachikulu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Koma iyeyo adaima pakatimpakati pa mundawo nautchinjiriza, ndipo adapha Afilistiwo, chifukwa Chauta adampambanitsa kwambiri. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Koma Sama anayima pakati pa mundawo. Iye anawuteteza nakantha Afilistiwo ndipo Yehova anawapambanitsa koposa. |
iye ananyamuka, nakantha Afilisti kufikira dzanja lake linalema, ndi dzanja lake lomamatika kulupanga; ndipo Yehova anachititsa chipulumutso chachikulu tsiku lija, ndipo anthu anabwera m'mbuyo mwake kukafunkha kokha.
Anali pamodzi ndi Davide ku Pasidamimu muja; Afilisti anasonkhanako kunkhondo kumene kunali munda wodzala ndi barele; ndipo anthu anathawa pamaso pa Afilisti.
Inu munapirikitsa amitundu ndi dzanja lanu, koma iwowa munawaoka; munasautsa mitundu ya anthu, ndipo munawaingitsa.