Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




2 Samueli 23:10 - Buku Lopatulika

10 iye ananyamuka, nakantha Afilisti kufikira dzanja lake linalema, ndi dzanja lake lomamatika kulupanga; ndipo Yehova anachititsa chipulumutso chachikulu tsiku lija, ndipo anthu anabwera m'mbuyo mwake kukafunkha kokha.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

10 iye ananyamuka, nakantha Afilisti kufikira dzanja lake linalema, ndi dzanja lake lomamatika kulupanga; ndipo Yehova anachititsa chipulumutso chachikulu tsiku lija, ndipo anthu anabwera m'mbuyo mwake kukafunkha kokha.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

10 Koma iyeyo adatsalira, nakantha Afilisti mpaka dzanja lake kuchita kutopa, komabe osataya lupanga. Tsiku limenelo Chauta adampambanitsa. Aisraelewo adabwerera pambuyo pake kudzangofunkha za ophedwawo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

10 Koma iye anayima osasuntha ndipo anakantha Afilisti mpaka mkono wake unatopa ndipo unakanirira ku lupanga lake. Yehova anapereka chigonjetso chachikulu pa tsiku limenelo. Asilikali anabwerera kwa Eliezara, kukatenga katundu wa anthu ophedwa.

Onani mutuwo Koperani




2 Samueli 23:10
20 Mawu Ofanana  

Koma iyeyo anaima pakati pamundawo, nautchinjiriza, napha Afilistiwo. Ndipo Yehova anachititsa chipulumutso chachikulu.


Ndipo Naamani kazembe wa khamu la nkhondo la mfumu ya Aramu anali munthu womveka pamaso pa mbuyake, ndi waulemu; popeza mwa iye Yehova adapulumutsa Aaramu; ndiyenso ngwazi, koma wakhate.


Anali pamodzi ndi Davide ku Pasidamimu muja; Afilisti anasonkhanako kunkhondo kumene kunali munda wodzala ndi barele; ndipo anthu anathawa pamaso pa Afilisti.


Mwa Mulungu tidzachita molimbika mtima: Ndipo Iye adzapondereza otisautsa.


Ndiye amene apatsa mafumu chipulumutso: Amene alanditsa Davide mtumiki wake kulupanga loipa.


Mafumu a magulu a ankhondo athawathawa, ndipo mkazi amene akhala kwao agawa zofunkha.


Chifukwa chake ndidzamgawira gawo ndi akulu; ndipo adzagawana ndi amphamvu zofunkha; pakuti Iye anathira moyo wake kuimfa; ndipo anawerengedwa pamodzi ndi olakwa; koma ananyamula machimo a ambiri, napembedzera olakwa.


Pakuti sindingathe kulimba mtima kulankhula zinthu zimene Khristu sanazichite mwa ine zakumveretsa anthu amitundu, ndi mau ndi ntchito,


Pakuti tilalikira si za ife tokha, koma Yesu Khristu Ambuye, ndi ife tokha akapolo anu, chifukwa cha Khristu.


Ndipo Yehova anawamwaza pamaso pa Israele, ndipo anawakantha makanthidwe aakulu ku Gibiyoni, nawapirikitsa panjira yokwera pa Betehoroni, nawakantha mpaka Azeka, ndi mpaka Makeda.


Ndipo Yoswa anagwira mafumu awa onse ndi dziko lao nthawi yomweyi; chifukwa Yehova Mulungu wa Israele anathirira Israele nkhondo.


Ndipo Yehova anawapereka m'dzanja la Israele, ndipo anawakantha, nawapirikitsa mpaka ku Sidoni waukulu, ndi ku Misirefoti-Maimu, ndi ku chigwa cha Mizipa ku m'mawa; nawakantha mpaka sanawasiyire ndi mmodzi yense.


Pamene anafika ku Lehi Afilisti anafuula pokomana naye; koma mzimu wa Yehova unamgwera kolimba, ndi zingwe zokhala pa manja ake zinanga thonje lopserera ndi moto, ndi zomangira zake zinanyotsoka pa manja ake.


Ndipo anamva ludzu lambiri, naitana kwa Yehova, nati, Mwapatsa Inu chipulumutso ichi chachikulu ndi dzanja la kapolo wanu; ndipo kodi ndife nalo ludzu tsopano ndi kugwa m'dzanja la osadulidwa awa?


Koma Saulo anati, Sadzaphedwa lero munthu; pakuti lero Yehova anachita chipulumutso mu Israele.


Chomwecho Yehova anapulumutsa Israele tsiku lija; ndipo nkhondo inapitirira pa Betaveni.


Ndipo Yonatani ananena ndi mnyamata wonyamula zida zake, Tiye tipite ku kaboma ka osadulidwa awa; kapena Yehova adzatigwirira ntchito; pakuti palibe chomletsa Yehova kupulumutsa angakhale ndi ambiri kapena ndi owerengeka.


Ndipo ana a Israele atathamangira Afilisti, anabwerera nafunkha za m'zithando zao.


popeza iye anataya moyo wake nakantha Mfilistiyo, ndipo Yehova anachitira Aisraele onse chipulumutso chachikulu, inu munachiona, nimunakondwera; tsono mudzachimwiranji mwazi wosalakwa, ndi kumupha Davide popanda chifukwa?


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa