Nenani kwa Mulungu, Ha, ntchito zanu nzoopsa nanga! Chifukwa cha mphamvu yanu yaikulu adani anu adzagonjera Inu.
2 Samueli 22:45 - Buku Lopatulika Alendo adzandigonjera ine, pakumva za ine, adzandimvera pomwepo. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Alendo adzandigonjera ine, pakumva za ine, adzandimvera pomwepo. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Anthu a maiko ena adabwera kwa ine kudzapemba; atangomva mau anga oyamba adandimvera. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Alendo amadzipereka okha pamaso panga; akangomva za ine, amandigonjera. |
Nenani kwa Mulungu, Ha, ntchito zanu nzoopsa nanga! Chifukwa cha mphamvu yanu yaikulu adani anu adzagonjera Inu.
Mlendo amene wadziphatika yekha kwa Yehova asanene, kuti, Yehova adzandilekanitsa ndithu ndi anthu ake; pena mfule asanene, Taonani ine ndili mtengo wouma.
Alendonso amene adziphatika okha kwa Yehova, kuti amtumikire Iye, ndi kukonda dzina la Yehova, akhale atumiki ake, yense amene asunga sabata osaliipitsa, nagwira zolimba chipangano changa;
Ndipo Simoni mwini wake anakhulupiriranso: ndipo m'mene anabatizidwa, anakhalira ndi Filipo; ndipo pakuona zizindikiro ndi mphamvu zazikulu zilikuchitika, anadabwa.
Wodala iwe, Israele; akunga iwe ndani, mtundu wa anthu opulumutsidwa ndi Yehova, ndiye chikopa cha thandizo lako, Iye amene akhala lupanga la ukulu wako! Ndi adani ako adzakugonjera; ndipo udzaponda pa misanje yao.