Ndipo pamene ana a Amoni anaona kuti Aaramu anathawa, iwonso anathawa pamaso pa Abisai, nalowa m'mzindamo. Ndipo Yowabu anabwera kuchokera kwa ana a Amoni, nafika ku Yerusalemu.
2 Samueli 22:38 - Buku Lopatulika Ndinapirikitsa adani anga, ndi kuwaononga; ndiponso sindinabwerere mpaka nditawatha. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndinapirikitsa adani anga, ndi kuwaononga; ndiponso sindinabwerera mpaka nditawatha. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ndidalondola adani anga ndi kuŵapeza, sindidabwerere mpaka nditaŵagonjetsa. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero “Ine ndinathamangitsa adani anga ndi kuwakantha; sindinabwerere mpaka iwo atawonongedwa. |
Ndipo pamene ana a Amoni anaona kuti Aaramu anathawa, iwonso anathawa pamaso pa Abisai, nalowa m'mzindamo. Ndipo Yowabu anabwera kuchokera kwa ana a Amoni, nafika ku Yerusalemu.
Ndipo ndinali nawe kulikonse unamukako, ndi kuononga adani ako onse pamaso pako; ndipo ndidzamveketsa dzina lako, monga dzina la akulu ali padziko lapansi.
Mdani anati, Ndiwalondola, ndiwapeza, ndidzagawa zofunkha; ndidzakhuta nao mtima; ndidzasolola lupanga langa, dzanja langa lidzawaononga.