2 Samueli 22:14 - Buku Lopatulika Yehova anagunda kumwamba; ndipo Wam'mwambamwamba ananena mau ake. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Yehova anagunda kumwamba; ndipo Wam'mwambamwamba ananena mau ake. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Kumwamba Chauta adagunda ngati bingu, Wopambanazonse liwu lake lidamveka. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Yehova anabangula kumwamba ngati bingu, mawu a Wammwambamwamba anamveka ponseponse. |
ndipo ndidzakuyesani ufumu wanga wa ansembe, ndi mtundu wopatulika. Awa ndi mau amene ukalankhule ndi ana a Israele.
Ndipo Yehova adzamveketsa mau ake a ulemerero, ndipo adzaonetsa kumenya kwa dzanja lake, ndi mkwiyo wake waukali, ndi lawi la moto wonyambita, ndi kuomba kwa mphepo, ndi mkuntho ndi matalala.
Ndipo mkokomo wa mapiko a akerubi unamveka mpaka bwalo lakunja, ngati mau a Mulungu Wamphamvuyonse, pakunena Iye.
Ndipo anatsegulidwa Kachisi wa Mulungu amene ali mu Mwamba; ndipo linaoneka likasa la chipangano chake, mu Kachisi mwake, ndipo panali mphezi, ndi mau, ndi mabingu, ndi chivomezi, ndi matalala aakulu.
Otsutsana ndi Yehova adzaphwanyika; kumwamba Iye adzagunda pa iwo; Yehova adzaweruza malekezero a dziko. Ndipo adzapatsa mphamvu mfumu yake, nadzakweza nyanga ya wodzozedwa wake.
Ndipo pamene Samuele analikupereka nsembe yopserezayo, Afilisti anayandikira kuti aponyane ndi Aisraele; koma tsiku lomwe lija Yehova anagunda ndi kugunda kwakukulu pa Afilistiwo, nawapolonganitsa. Ndipo anakanthidwa pamaso pa Aisraele.