Ndipo anapyola mafuko onse a Israele kufikira ku Abele ndi ku Betimaaka, ndi kwa Abikiri onse; iwo nasonkhana pamodzi namlondolanso.
2 Samueli 20:15 - Buku Lopatulika Ndipo anadza nammangira misasa mu Abele wa Betimaaka, naundira nthumbira pa mzindawo, ndipo unagunda linga; ndipo anthu onse akukhala ndi Yowabu anakumba lingalo kuti aligwetse. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo anadza nammangira misasa m'Abele wa Betimaaka, naundira nthumbira pa mudziwo, ndipo unagunda linga; ndipo anthu onse akukhala ndi Yowabu anakumba lingalo kuti aligwetse. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ndipo anthu onse amene anali ndi Yowabu adabwera, nadzamzinga ndi zithando zankhondo Shebayo ku Abele wa ku Betemaki. Tsono adauundira mitumbira yankhondo mzindawo, nikagunda ku linga. Choncho ankagumula khoma kuti aligwetse. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ankhondo onse pamodzi ndi Yowabu anafika ndi kumuzungulira Seba mu Abeli-Beti-Maaka. Iwo anapanga mzere wa nkhondo mpaka ku mzinda, ndipo unayangʼanana ndi malo otetezera a kunja. Pamene amalimbana ndi khoma kuti aligwetse, |
Ndipo anapyola mafuko onse a Israele kufikira ku Abele ndi ku Betimaaka, ndi kwa Abikiri onse; iwo nasonkhana pamodzi namlondolanso.
Ndipo Benihadadi anamvera mfumu Asa, natuma akazembe a nkhondo ake kukathira nkhondo kumizinda ya Israele, napasula Iyoni, ndi Dani, ndi Abele-Beti-Maaka, ndi Kineroti wonse, ndi dziko lonse la Nafutali.
Masiku a Peka mfumu ya Israele anadza Tigilati-Pilesere mfumu ya Asiriya, nalanda Iyoni, ndi Abele-Beti-Maaka, ndi Yanowa, ndi Kedesi, ndi Hazori, ndi Giliyadi, ndi Galileya, dziko lonse la Nafutali; nawatenga andende kunka nao ku Asiriya.
Chifukwa chake atero Yehova za mfumu ya Asiriya, Iye sadzalowa m'mzinda muno, kapena kuponyamo muvi, kapena kufikako ndi chikopa, kapena kuundira mtumbira.
panali mzinda waung'ono muli anthu owerengeka; ndipo inadzako mfumu yaikulu, nawuzinga ndi nkhondo, nkumanga malinga aakulu;
Chifukwa chake atero Yehova za mfumu ya Asiriya, Iye sadzafika mu mzinda muno, ngakhale kuponyapo muvi, ngakhale kufika patsogolo pake ndi chikopa, ngakhale kuunjikirapo mulu.
taonani mitumbira, yafika kumzinda kuugwira, ndipo mzinda uperekedwa m'dzanja la Ababiloni olimbana nao, chifukwa cha lupanga, ndi chifukwa cha njala, ndi chifukwa cha mliri; ndipo chimene munachinena chaoneka; ndipo, taonani, muchiona.
Pakuti atero Yehova, Mulungu wa Israele, za nyumba za mzinda uno, ndi za nyumba za mafumu a Yuda'zi, zinagwetsedwa ziwatchinjirizire mitumbira, ndi lupanga:
Pakuti Yehova wa makamu atero, Dulani mitengo, unjikani nthumbira pomenyana ndi Yerusalemu; mzinda wakudzalangidwa ndi uwu; m'kati mwake modzala nsautso.
nuuzinge, nuumangire nsanja zouzinga, nuundire nthumbira, ndi kuumangira misasa, nuuikire zogumulira pozungulira pake.
Pakuti masiku adzakudzera, ndipo adani ako adzakuzingira linga, nadzakuzungulira iwe kwete, nadzakutsekereza ponsepo;