Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yeremiya 6:6 - Buku Lopatulika

6 Pakuti Yehova wa makamu atero, Dulani mitengo, unjikani nthumbira pomenyana ndi Yerusalemu; mzinda wakudzalangidwa ndi uwu; m'kati mwake modzala nsautso.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

6 Pakuti Yehova wa makamu atero, Dulani mitengo, unjikani nthumbira pomenyana ndi Yerusalemu; mudzi wakudzalangidwa ndi uwu; m'kati mwake modzala nsautso.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

6 Mau a Chauta Wamphamvuzonse akuti, “Gwetsani mitengo ya mu Yerusalemu, ndipo mzindawu muumangire nthumbira zankhondo. Mzinda umenewu ndi woyenera kulangidwa, anthu ake amangokhalira kuzunzana.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

6 Yehova Wamphamvuzonse akuti, “Dulani mitengo ndipo mumange mitumbira yankhondo kulimbana ndi Yerusalemu. Mzinda umenewu uyenera kulangidwa; wadzaza ndi kuponderezana.

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 6:6
15 Mawu Ofanana  

Chifukwa chake atero Yehova za mfumu ya Asiriya, Iye sadzafika mu mzinda muno, ngakhale kuponyapo muvi, ngakhale kufika patsogolo pake ndi chikopa, ngakhale kuunjikirapo mulu.


Pakuti paliponse ndinena, ndifuula; ndifuula, Chiwawa ndi chofunkha; pakuti mau a Yehova ayesedwa kwa ine chitonzo, ndi choseketsa, dzuwa lonse.


Koma maso ako ndi mtima wako sizisamalira kanthu koma kusirira, ndi kukhetsa mwazi wosachimwa, ndi kusautsa, ndi zachiwawa, kuti uzichite.


taonani mitumbira, yafika kumzinda kuugwira, ndipo mzinda uperekedwa m'dzanja la Ababiloni olimbana nao, chifukwa cha lupanga, ndi chifukwa cha njala, ndi chifukwa cha mliri; ndipo chimene munachinena chaoneka; ndipo, taonani, muchiona.


Pakuti mzinda uwu unali woutsa mkwiyo wanga ndi ukali wanga kuyambira tsiku lija anaumanga mpaka lero, kuti ndiuchotse pamaso panga;


Pakuti atero Yehova, Mulungu wa Israele, za nyumba za mzinda uno, ndi za nyumba za mafumu a Yuda'zi, zinagwetsedwa ziwatchinjirizire mitumbira, ndi lupanga:


Chaka chachisanu ndi chinai cha Zedekiya mfumu ya Yuda, mwezi wakhumi, anadza Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni ndi nkhondo yake yonse ku Yerusalemu, ndi kuumangira misasa.


Sindidzawalanga kodi chifukwa cha zimenezi? Ati Yehova; kodi moyo wanga sudzabwezera chilango mtundu wotere?


Kodi sindidzawalanga chifukwa cha zimenezi? Ati Yehova; kodi moyo wanga sudzabwezera chilango mtundu woterewu?


nuuzinge, nuumangire nsanja zouzinga, nuundire nthumbira, ndi kuumangira misasa, nuuikire zogumulira pozungulira pake.


Atero Yehova Mulungu, Uwu ndi Yerusalemu ndinauika pakati pa amitundu, ndi pozungulira pake pali maiko.


Ndi mfumu ya kumpoto idzadza, nidzaunda mtumbira, nidzalanda mizinda yamalinga; ndi ankhondo a kumwera sadzalimbika, ngakhale anthu ake osankhika; inde sipadzakhala mphamvu yakulimbika.


Tsoka uyo wopanduka, ndi wodetsedwa, ndiye mzinda wozunza!


Pakuti masiku adzakudzera, ndipo adani ako adzakuzingira linga, nadzakuzungulira iwe kwete, nadzakutsekereza ponsepo;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa