Koma Yowabu ndi Abisai anampirikitsa Abinere; ndipo dzuwa linawalowera pofika ku chitunda cha Ama, chakuno cha Giya, panjira ya ku chipululu cha Gibiyoni.
2 Samueli 2:23 - Buku Lopatulika Koma iye anakana kupatuka; chifukwa chake Abinere anamkantha ndi mutu wa mkondo m'mimba mwake, ndi mutuwo unatuluka kumbuyo kwake. Ndipo anagwako, nafera pomwepo. Ndipo onse akufika kumalo kumene Asahele anagwa, namwalirapo, anaima pomwepo. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Koma iye anakana kupatuka; chifukwa chake Abinere anamkantha ndi khali la mkondo m'mimba mwake, ndi khalilo linatuluka kumbuyo kwake. Ndipo anagwako, nafera pomwepo. Ndipo onse akufika kumalo kumene Asahele anagwa, namwalirapo, anaima pomwepo. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Koma Asahele sadafune kumleka. Choncho Abinere adabaya Asaheleyo m'mimba ndi luti la mkondo wake, mkondowo nkutulukira kumsana. Asahele adagwa pansi, kufa nkukhala komweko. Anthu onse amene adafika pamalo pomwe padafera Asahele, adangoima kungoti kakasi. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Koma iye anakana kuleka kumuthamangitsa. Choncho Abineri anabaya Asaheli mʼmimba ndi msonga ya mkondo wake ndipo mkondowo unatulukira mbali ina. Iye anagwa ndi kufera pamalo pomwepo. Ndipo munthu aliyense amayima akafika pamalo pamene anagwera ndi kufa. |
Koma Yowabu ndi Abisai anampirikitsa Abinere; ndipo dzuwa linawalowera pofika ku chitunda cha Ama, chakuno cha Giya, panjira ya ku chipululu cha Gibiyoni.
Koma Amasa sanasamalire lupanga lili m'dzanja la Yowabu; chomwecho iye anamgwaza nalo m'mimba; nakhuthula matumbo ake pansi, osamgwazanso, nafa iye. Ndipo Yowabu ndi Abisai mbale wake analondola Sheba mwana wa Bikiri.
Pofikanso Abinere ku Hebroni, Yowabu anampambutsa kupita naye pakati pa chipata kulankhula naye poduka mphepo; namgwaza pomwepo m'mimba, nafa, chifukwa cha mwazi wa Asahele mbale wake.
Motero Yowabu ndi Abisai mbale wake adapha Abinere, popeza iye adapha mbale wao Asahele ku Gibiyoni, kunkhondo.
Ndipo iwo analowanso kufikira m'kati mwa nyumba, monga ngati anadzatenga tirigu; namgwaza m'mimba mwake; ndi Rekabu ndi Baana mbale wake anathawa.
Ndipo mfumu ndi anthu ake anamuka ku Yerusalemu kuyambana nao Ayebusi, nzika za dziko; ndiwo ananena kwa Davide ndi kuti, Sudzalowa muno, koma akhungu ndi opunduka adzakupirikitsa; ndiko kunena kuti, Davide sangathe kulowa muno.