Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Samueli 2:23 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

23 Koma iye anakana kuleka kumuthamangitsa. Choncho Abineri anabaya Asaheli mʼmimba ndi msonga ya mkondo wake ndipo mkondowo unatulukira mbali ina. Iye anagwa ndi kufera pamalo pomwepo. Ndipo munthu aliyense amayima akafika pamalo pamene anagwera ndi kufa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

23 Koma iye anakana kupatuka; chifukwa chake Abinere anamkantha ndi mutu wa mkondo m'mimba mwake, ndi mutuwo unatuluka kumbuyo kwake. Ndipo anagwako, nafera pomwepo. Ndipo onse akufika kumalo kumene Asahele anagwa, namwalirapo, anaima pomwepo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

23 Koma iye anakana kupatuka; chifukwa chake Abinere anamkantha ndi khali la mkondo m'mimba mwake, ndi khalilo linatuluka kumbuyo kwake. Ndipo anagwako, nafera pomwepo. Ndipo onse akufika kumalo kumene Asahele anagwa, namwalirapo, anaima pomwepo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

23 Koma Asahele sadafune kumleka. Choncho Abinere adabaya Asaheleyo m'mimba ndi luti la mkondo wake, mkondowo nkutulukira kumsana. Asahele adagwa pansi, kufa nkukhala komweko. Anthu onse amene adafika pamalo pomwe padafera Asahele, adangoima kungoti kakasi.

Onani mutuwo Koperani




2 Samueli 2:23
7 Mawu Ofanana  

Koma Yowabu ndi Abisai anathamangitsa Abineri, ndipo dzuwa likulowa, anafika ku phiri la Ama, pafupi ndi Giya pa njira yopita ku chipululu cha ku Gibiyoni.


Amasa sanayangʼanitsitse lupanga limene linali mʼdzanja la Yowabu, ndipo Yowabu anamubaya nalo mʼmimba ndipo matumbo ake anatuluka ndi kugwera pansi. Popanda kubayanso kachiwiri, Amasa anafa. Ndipo Yowabu ndi mʼbale wake Abisai anathamangitsa Seba mwana wa Bikiri.


Tsono Abineri atabwerera ku Hebroni, Yowabu anamutengera pambali ku chipata, kukhala ngati akufuna kuyankhula naye mwamseri. Ndipo kumeneko pobwezera imfa ya mʼbale wake Asaheli, Yowabu analasa iyeyo mʼmimba, ndipo anafa.


(Yowabu ndi mʼbale wake Abisai anapha Abineri chifukwa iye anapha mʼbale wawo Asaheli ku nkhondo ku Gibiyoni).


Iwo analowa mʼchipinda chamʼkati ngati kuti amakatenga tirigu, ndipo anamulasa mʼmimba. Kenaka Rekabu ndi mʼbale wake Baana anathawa.


Mfumu ndi ankhondo ake anapita ku Yerusalemu kukathira nkhondo Ayebusi amene ankakhala kumeneko. Ayebusiwo anamuwuza Davide kuti, “Inu simulowa muno. Ngakhale osaona ndi olumala akhoza kukuthamangitsani.” Iwo ankaganiza kuti, “Davide sangathe kulowa momwemo.”


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa