Ndipo Abinere ananena naye, Patuka iwe kulamanja kapena kulamanzere kwako nudzigwirire wina wa anyamatawo, nutenge zida zake. Koma Asahele anakana kupatuka pakumtsata iye.
2 Samueli 2:22 - Buku Lopatulika Ndipo Abinere anabwereza kunena kwa Asahele, Patuka pakunditsata ine. Ndidzakukanthiranji kukugwetsa pansi? Ndikatero ndidzaweramutsanso bwanji nkhope yanga kwa mbale wako Yowabu? Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Abinere anabwereza kunena kwa Asahele, Patuka pakunditsata ine. Ndidzakukanthiranji kukugwetsa pansi? Ndikatero ndidzaweramutsanso bwanji nkhope yanga kwa mbale wako Yowabu? Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono Abinere adauzanso Asahele kuti, “Iwe leke, usandithamangitse, bwanji ukundikakamiza kuti ndikuphe? Nanga ndikakupha, mbale wako Yowabu ndikaonana naye bwanji?” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Abineri anamuchenjezanso Asaheli, “Siya kuthamangitsa ine! Kodi ndikukanthe chifukwa chiyani? Kodi ndikaonana naye bwanji mʼbale wako Yowabu?” |
Ndipo Abinere ananena naye, Patuka iwe kulamanja kapena kulamanzere kwako nudzigwirire wina wa anyamatawo, nutenge zida zake. Koma Asahele anakana kupatuka pakumtsata iye.
Pofikanso Abinere ku Hebroni, Yowabu anampambutsa kupita naye pakati pa chipata kulankhula naye poduka mphepo; namgwaza pomwepo m'mimba, nafa, chifukwa cha mwazi wa Asahele mbale wake.
Yemwe aumitsa khosi atadzudzulidwa kwambiri, adzasweka modzidzimuka, palibe chomchiritsa.
Chomwe chinalipo chatchedwa dzina lake kale, chidziwika kuti ndiye munthu; sangathe kulimbana ndi womposa mphamvu.
Nati Saulo kwa Mikala, Wandinyengeranji chomwechi, ndi kulola mdani wanga apulumuke? Ndipo Mikala anayankha Saulo, Iye anati kwa ine, Undilole ndipite, ndingakuphe.