Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Samueli 2:22 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

22 Abineri anamuchenjezanso Asaheli, “Siya kuthamangitsa ine! Kodi ndikukanthe chifukwa chiyani? Kodi ndikaonana naye bwanji mʼbale wako Yowabu?”

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

22 Ndipo Abinere anabwereza kunena kwa Asahele, Patuka pakunditsata ine. Ndidzakukanthiranji kukugwetsa pansi? Ndikatero ndidzaweramutsanso bwanji nkhope yanga kwa mbale wako Yowabu?

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

22 Ndipo Abinere anabwereza kunena kwa Asahele, Patuka pakunditsata ine. Ndidzakukanthiranji kukugwetsa pansi? Ndikatero ndidzaweramutsanso bwanji nkhope yanga kwa mbale wako Yowabu?

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

22 Tsono Abinere adauzanso Asahele kuti, “Iwe leke, usandithamangitse, bwanji ukundikakamiza kuti ndikuphe? Nanga ndikakupha, mbale wako Yowabu ndikaonana naye bwanji?”

Onani mutuwo Koperani




2 Samueli 2:22
6 Mawu Ofanana  

Ndipo Abineri anati kwa iye, “Khotera kumanja kapena kumanzere: tsatira mmodzi mwa anyamatawa ndipo umulande zida zake.” Koma Asaheli sanasiye kumuthamangitsa.


Tsono Abineri atabwerera ku Hebroni, Yowabu anamutengera pambali ku chipata, kukhala ngati akufuna kuyankhula naye mwamseri. Ndipo kumeneko pobwezera imfa ya mʼbale wake Asaheli, Yowabu analasa iyeyo mʼmimba, ndipo anafa.


Munthu amene amawumitsabe khosi lake atadzudzulidwa kwambiri, adzawonongeka mwadzidzidzi popanda chomuchiritsa.


Chilichonse chimene chilipo anachitchula kale dzina, za mmene munthu alili nʼzodziwika; sangathe kutsutsana ndi munthu amene ali wamphamvu kupambana iyeyo.


Tsono Sauli anafunsa Mikala kuti, “Nʼchifukwa chiyani wandinamiza chotere polola kuti mdani wanga athawe?” Mikala anayankha kuti, “Davide anandiwuza kuti, ‘Ukapanda kutero ndikupha.’ ”


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa