Chifukwa chake tsono lupanga silidzachoka pa nyumba yako nthawi zonse, popeza unandipeputsa Ine, nudzitengera mkazi wa Uriya Muhiti akhale mkazi wako.
2 Samueli 18:15 - Buku Lopatulika Ndipo anyamata khumi onyamula zida zake za Yowabu anamzungulira Abisalomu namkantha namupha. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo anyamata khumi onyamula zida zake za Yowabu anamzungulira Abisalomu namkantha namupha. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pomwepo ankhondo khumi onyamula zida zankhondo za Yowabu, adazinga Abisalomu, namkantha mpaka kumupha. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndipo anthu khumi onyamula zida za Yowabu anazungulira Abisalomu, kumubaya ndi kumupha. |
Chifukwa chake tsono lupanga silidzachoka pa nyumba yako nthawi zonse, popeza unandipeputsa Ine, nudzitengera mkazi wa Uriya Muhiti akhale mkazi wako.
Pomwepo Yowabu anati, Sindiyenera kuchedwa nawe. Natenga mikondo itatu nagwaza nayo mtima wa Abisalomu alikukhala wamoyo pakati pa mtengowo.
Ndipo Yowabu analiza lipenga, ndipo anthu anabwerera naleka kupirikitsa Aisraele; pakuti Yowabu analetsa anthuwo.
Ndipo mfumu Davide anatumiza kwa Zadoki ndi Abiyatara ansembewo, nati, Mulankhule nao akulu a Yuda, kuti, Mukhale bwanji am'mbuyo kubwera nayo mfumu kunyumba yake? Pakuti mau a Aisraele onse anafika kwa mfumu akuti abwere nayo kunyumba yake.
kuti kufuula kokondwera kwa woipa sikukhalira kutha, ndi chimwemwe cha wonyoza Mulungu chikhala kamphindi?