Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Mlaliki 10:8 - Buku Lopatulika

8 Wokumba mbuna adzagwamo; ndipo woboola mpanda njoka idzamluma.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

8 Wokumba mbuna adzagwamo; ndipo woboola mpanda njoka idzamluma.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

8 Amene amakumba dzenje adzagwamo yekha. Amene amaboola khoma njoka idzamuluma.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

8 Amene amakumba dzenje adzagwamo yekha; amene amabowola khoma adzalumidwa ndi njoka.

Onani mutuwo Koperani




Mlaliki 10:8
13 Mawu Ofanana  

Ndipo Ahitofele, pakuona kuti sautsata uphungu wake anamanga bulu wake, nanyamuka, nanka kumzinda kwao, nakonza za pa banja lake, nadzipachika, nafa, naikidwa m'manda a atate wake.


Ndipo anyamata khumi onyamula zida zake za Yowabu anamzungulira Abisalomu namkantha namupha.


Nampachika Hamani pa mtengo adaukonzera Mordekai. Pamenepo mkwiyo wa mfumu unatsika.


Ananditchera ukonde apo ndiyenda; moyo wanga wawerama. Anandikumbira mbuna patsogolo panga; anagwa m'kati mwake iwo okha.


Chilungamo cha oongoka mtima chidzawapulumutsa; koma achiwembu adzagwidwa ndi mphulupulu yao.


Wokumba dzenje adzagwamo, wogubuduza mwala, udzabweranso pa iye mwini.


Wosendeza miyala adzaphwetekedwa nayo; wowaza nkhuni nadzitema.


Kudzakhala monga munthu akathawa mkango, ndi chimbalangondo chikomana naye; kapena akalowa m'nyumba, natsamira kukhoma ndi dzanja lake, nimluma njoka.


Angakhale abisala pamwamba pa Karimele, ndidzawapwaira ndi kuwatenga komweko; angakhale abisala pamaso panga pansi pa nyanja, kumeneko ndidzalamulira njoka, ndipo idzawaluma.


Ndipo anamuka kunyumba ya atate wake ku Ofura, nawapha abale ake ana a Yerubaala, ndiwo amuna makumi asanu ndi awiri, pa thanthwe limodzi; koma Yotamu mwana wamng'ono wa Yerubaala anatsalako; pakuti anabisala.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa