Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




2 Samueli 19:11 - Buku Lopatulika

11 Ndipo mfumu Davide anatumiza kwa Zadoki ndi Abiyatara ansembewo, nati, Mulankhule nao akulu a Yuda, kuti, Mukhale bwanji am'mbuyo kubwera nayo mfumu kunyumba yake? Pakuti mau a Aisraele onse anafika kwa mfumu akuti abwere nayo kunyumba yake.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

11 Ndipo mfumu Davide anatumiza kwa Zadoki ndi Abiyatara ansembewo, nati, Mulankhule nao akulu a Yuda, kuti, Mukhale bwanji am'mbuyo kubwera nayo mfumu kunyumba yake? Pakuti mau a Aisraele onse anafika kwa mfumu akuti abwere nayo kunyumba yake.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

11 Mfumu Davide adatumiza mau kwa ansembe aja, Zadoki ndi Abiyatara, akuti, “Mufunse atsogoleri a ku Yuda kuti, ‘Chifukwa chiyani inu mukuzengereza kwambiri osakaitenganso mfumu kuti ibwerere ku nyumba kwake, pamene Aisraele onse atumiza kale mau kwa mfumu onena kuti mfumu ibwerere kunyumba kwake?

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

11 Mfumu Davide inatumiza uthenga uwu kwa ansembe Zadoki ndi Abiatara, “Funsani akuluakulu a Yuda, ‘Nʼchifukwa chiyani inu mukukhala otsiriza kuyitana mfumu ku nyumba yake yaufumu, pakuti zimene zikunenedwa mu Israeli yense zamveka kwa mfumu ndi onse amene akukhala nayo.

Onani mutuwo Koperani




2 Samueli 19:11
11 Mawu Ofanana  

Chifukwa chake Zadoki ndi Abiyatara ananyamulanso likasa la Mulungu nafika nalo ku Yerusalemu. Ndipo iwo anakhala kumeneko.


Pomwepo Yowabu anati, Sindiyenera kuchedwa nawe. Natenga mikondo itatu nagwaza nayo mtima wa Abisalomu alikukhala wamoyo pakati pa mtengowo.


Ndipo anyamata khumi onyamula zida zake za Yowabu anamzungulira Abisalomu namkantha namupha.


Ndipo Abisalomu amene tinamdzoza mfumu yathu anafa kunkhondo. Chifukwa chake tsono mulekeranji kunena mau akuti abwere nayo mfumuyo?


Ndipo onani, Aisraele onse anafika kwa mfumu, nanena ndi mfumu, Abale athu anthu a Yuda anakuchotsani bwanji mwakuba, naolotsa mfumu ndi banja lake pa Yordani, ndi anthu onse a Davide pamodzi naye?


Ndipo mfumu inaika Benaya mwana wa Yehoyada m'malo mwake kutsogolera khamu la nkhondo, ndi mfumu inaika Zadoki wansembe m'malo mwa Abiyatara.


Chomwecho muwalitse inu kuunika kwanu pamaso pa anthu, kuti pakuona ntchito zanu zabwino, alemekeze Atate wanu wa Kumwamba.


Chifukwa chake tili atumiki m'malo mwa Khristu, monga ngati Mulungu alikudandaulira mwa ife; tiumiriza inu m'malo mwa Khristu, yanjanitsidwani ndi Mulungu.


si chifukwa tilibe ulamuliro, komatu kuti tidzipereke tokha tikhale kwa inu chitsanzo chanu, kuti mukatitsanze ife.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa