Ndipo uphungu wa Ahitofele anaupangira masiku aja, unali monga ngati munthu anafunsira mau kwa Mulungu; uphungu wonse wa Ahitofele unali wotere kwa Davide ndi kwa Abisalomu yemwe.
2 Samueli 17:1 - Buku Lopatulika Ndipo Ahitofele ananena ndi Abisalomu, Ndiloleni ndisankhe tsopano anthu zikwi khumi ndi ziwiri, ndipo ndidzanyamuka usiku womwe uno ndi kulondola Davide; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Ahitofele ananena ndi Abisalomu, Ndiloleni ndisankhe tsopano anthu zikwi khumi ndi ziwiri, ndipo ndidzanyamuka usiku womwe uno ndi kulondola Davide; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pambuyo pake Ahitofele adauza Abisalomu kuti, “Mundilole ndisankhule anthu okwanira 12,000, ndinyamuke nawo kuti ndimthamangire Davide usiku uno. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ahitofele anati kwa Abisalomu, “Mundilole ndisankhe asilikali 12,000, ndinyamuke usiku womwe uno kuti ndithamangire Davide. |
Ndipo uphungu wa Ahitofele anaupangira masiku aja, unali monga ngati munthu anafunsira mau kwa Mulungu; uphungu wonse wa Ahitofele unali wotere kwa Davide ndi kwa Abisalomu yemwe.
ndipo ndidzamgwera ali wolema ndi wofooka, ndi kumuopsa; ndi anthu onse amene ali naye adzathawa; pamenepo ndidzakantha mfumu yokha;
Ndi mtendere ndidzagona pansi, pomwepo ndidzagona tulo; chifukwa Inu, Yehova, mundikhalitsa ine, ndikhale bwino.
Pakuti akapanda kuchita zoipa, samagona; ndipo akapanda kukhumudwitsa wina, tulo tao tiwachokera.