Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




2 Samueli 16:23 - Buku Lopatulika

23 Ndipo uphungu wa Ahitofele anaupangira masiku aja, unali monga ngati munthu anafunsira mau kwa Mulungu; uphungu wonse wa Ahitofele unali wotere kwa Davide ndi kwa Abisalomu yemwe.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

23 Ndipo uphungu wa Ahitofele anaupangira masiku aja, unali monga ngati munthu anafunsira mau kwa Mulungu; uphungu wonse wa Ahitofele unali wotere kwa Davide ndi kwa Abisalomu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

23 Tsono masiku amenewo, malangizo amene ankapereka Ahitofele anali ngati mau ochokera kwa Mulungu. Choncho uphungu wonse wa Ahitofele ankaulemekeza Davide ndi Abisalomu yemwe.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

23 Tsono masiku amenewo malangizo amene Ahitofele amapereka anali ngati mawu ochokera kwa Mulungu. Umu ndi mmene Davide ndi Abisalomu amalandirira malangizo onse a Ahitofele.

Onani mutuwo Koperani




2 Samueli 16:23
20 Mawu Ofanana  

Ndipo Abisalomu anaitana Ahitofele Mgiloni, phungu wa Davide, kumzinda wake ndiwo Gilo, pamene iye analikupereka nsembe. Ndipo chiwembucho chinali cholimba; pakuti anthu anachulukachulukabe kwa Abisalomu.


Ndipo wina anauza Davide nati, Ahitofele ali pakati pa opangana chiwembu pamodzi ndi Abisalomu. Davide nati, Yehova, musandulize uphungu wa Ahitofele ukhale wopusa.


Ndipo Ahitofele ananena ndi Abisalomu, Ndiloleni ndisankhe tsopano anthu zikwi khumi ndi ziwiri, ndipo ndidzanyamuka usiku womwe uno ndi kulondola Davide;


Ndipo Abisalomu ndi anthu onse a Israele anati, Uphungu wa Husai Mwariki uposa uphungu wa Ahitofele. Pakuti kunaikidwa ndi Yehova kutsutsa uphungu wabwino wa Ahitofele kuti Yehova akamtengere Abisalomu choipa.


Ndipo Ahitofele, pakuona kuti sautsata uphungu wake anamanga bulu wake, nanyamuka, nanka kumzinda kwao, nakonza za pa banja lake, nadzipachika, nafa, naikidwa m'manda a atate wake.


Koma kwa munthu anati, Taonani, kuopa Ambuye ndiko nzeru; ndi kupatukana nacho choipa ndiko luntha.


Apititsa pachabe ziwembu za ochenjera, kuti manja ao sangathe kuchita chopangana chao.


Malamulo a Yehova ali angwiro, akubwezera moyo; mboni za Yehova zili zokhazikika, zakuwapatsa opusa nzeru.


Mverani mau a kupemba kwanga, pamene ndilirira Inu, pamene ndikweza manja anga kuloza ponenera panu poyera.


Ntchentche zakufa zinunkhitsa moipa ndipo zioletsa mafuta onunkhira a sing'anga; chomwecho kupusa kwapang'ono kuipitsa iye amene atchuka chifukwa cha nzeru ndi ulemu.


Pakuti anthu anga apusa, sandidziwa Ine; ali ana opulukira sazindikira; ali ochenjera kuchita choipa koma kuchita chabwino sakudziwa.


Anzeru ali ndi manyazi, athedwa nzeru nagwidwa; taonani, akana mau a Yehova; ali nayo nzeru yotani?


Ndipo aime pamaso pa Eleazara wansembe, amene amfunsire monga mwa chiweruzo cha Urimu pamaso pa Yehova; ponena iye azituluka, ndi ponena iye azilowa, ndi iye ndi ana onse a Israele pamodzi naye, ndiwo khamu lonse.


Nyengo imeneyo Yesu anayankha nati, Ndivomerezana ndi Inu, Atate, Ambuye wakumwamba ndi dziko lapansi, kuti munazibisira izo kwa anzeru ndi akudziwitsa, ndipo munaziululira zomwe kwa makanda:


Ndipo mbuye wake anatama kapitao wonyengayo, kuti anachita mwanzeru; chifukwa ana a nthawi ya pansi pano ali anzeru m'mbadwo wao koposa ana a kuunika.


Pakunena kuti ali anzeru, anapusa;


akalankhula wina, alankhule ngati manenedwe a Mulungu; wina akatumikira, achite ngati mu mphamvu imene Mulungu ampatsa, kuti m'zonse Mulungu alemekezedwe mwa Yesu Khristu, amene ali nao ulemerero ndi mphamvu kunthawi za nthawi. Amen.


Ndipo Davide anafunsira kwa Yehova, nati, Ndikalondola khamulo ndidzalipeza kodi? Ndipo anamyankha kuti, Londola, pakuti zoonadi udzawapeza, ndi kulanditsa zonse.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa