Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




2 Samueli 16:22 - Buku Lopatulika

22 Chomwecho iwo anayalira Abisalomu hema pamwamba pa nyumba; ndipo Abisalomu analowa kwa akazi aang'ono a atate wake pamaso pa Aisraele onse.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

22 Chomwecho iwo anayalira Abisalomu hema pamwamba pa nyumba; ndipo Abisalomu analowa kwa akazi aang'ono a atate wake pamaso pa Aisraele onse.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

22 Motero adamangira Abisalomu hema pa denga la nyumba ya mfumu. Ndipo Abisalomu adapita kukaloŵa kwa azikazi a bambo wake, Aisraele onse akupenya.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

22 Choncho anamangira tenti Abisalomu pa denga la nyumba ndipo iye anagona ndi azikazi a abambo ake Aisraeli onse akuona.

Onani mutuwo Koperani




2 Samueli 16:22
11 Mawu Ofanana  

Ndipo panali pamene Israele anakhala m'dzikomo, Rubeni anamuka nagona ndi Biliha, mkazi wamng'ono wa atate wake: ndipo Israele anamva. Ana aamuna a Yakobo anali khumi ndi awiri:


Ndipo kunali pa madzulo Davide anauka pa kama wake nayenda pa tsindwi la nyumba ya mfumu. Ndipo iye ali patsindwipo anaona mkazi alinkusamba; ndi mkaziyo anali wochititsa kaso pomuyang'ana.


Mfumu nituluka, ndi banja lake lonse linamtsata. Ndipo mfumu inasiya akazi khumi ndiwo akazi aang'ono, kusunga nyumbayo.


Ndipo Davide anafika kunyumba kwake ku Yerusalemu. Mfumuyo nitenga akazi khumi aang'onowo amene adawasiya asunge nyumbayo, nawatsekera m'nyumba, nawapatsa chakudya, koma sanalowane nao. Chomwecho iwowa anatsekedwa kufikira tsiku la imfa yao, nakhala ngati akazi amasiye.


Maonekedwe a nkhope zao awachitira iwo mboni; ndipo amaonetsa uchimo wao monga Sodomu, saubisa. Tsoka kwa moyo wao! Chifukwa iwo anadzichitira zoipa iwo okha.


Ndipo mvula yakanidwa, ndipo panalibe mvula ya masika; ndipo unali ndi nkhope ya mkazi wadama, unakana manyazi.


Kodi anakhala ndi manyazi pamene anachita zonyansa? Iai, sanakhale ndi manyazi, sananyale; chifukwa chake adzagwa mwa iwo amene akugwa, nthawi ya kuyang'aniridwa kwao adzagwetsedwa, ati Yehova.


Pakuti mwazi wake uli m'kati mwake anauika pathanthwe poyera, sanautsanulire panthaka kuukwirira ndi fumbi.


Ndipo, taonani, anadza wina wa ana a Israele, nabwera naye mkazi Mmidiyani kudza naye kwa abale ake, pamaso pa Mose, ndi pamaso pa khamu lonse la ana a Israele, pakulira iwo pa khomo la chihema chokomanako.


chitsiriziro chao ndicho kuonongeka, mulungu wao ndiyo mimba yao, ulemerero wao uli m'manyazi ao, amene alingirira za padziko.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa