2 Samueli 15:6 - Buku Lopatulika Abisalomu anachitira zotero Aisraele onse akudza kwa mfumu kuti aweruze mlandu wao; chomwecho Abisalomu anakopa mitima ya anthu a Israele. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Abisalomu anachitira zotero Aisraele onse akudza kwa mfumu kuti aweruze mlandu wao; chomwecho Abisalomu anakopa mitima ya anthu a Israele. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Umu ndimo m'mene Abisalomu ankachitira ndi Aisraele onse amene ankabwera kwa mfumu kuti akaweruzidwe. Motero Abisalomu adaŵagwira mitima Aisraele. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Abisalomu amachitira izi Aisraeli onse amene amabwera kwa mfumu kuti adzaweruzidwe ndipo Abisalomuyo anagwira mtima anthu a mu Israeli. |
Wonyoza Mulungu aononga mnzake ndi m'kamwa mwake; koma olungama adzapulumuka pakudziwa.
Ndinapenyera anthu onse amoyo akuyenda kunja kuno, kuti anali ndi mwana, wachiwiri, amene adzalowa m'malo mwake.
Ndi m'malo mwake adzauka munthu woluluka, amene anthu sanampatse ulemu wa ufumu, koma adzafika kachetechete, nadzalanda ufumu ndi mau osyasyalika.
Pakuti otere satumikira Ambuye wathu Khristu, koma mimba yao; ndipo ndi mau osalaza ndi osyasyalika asocheretsa mitima ya osalakwa.
Ndipo m'chisiriro adzakuyesani malonda ndi mau onyenga; amene chiweruzo chao sichinachedwe ndi kale lomwe, ndipo chitayiko chao sichiodzera.