Chifukwa chake tsono chakuti ndadzanena mau awa ndi mbuye wanga mfumu, ndicho kuti anthu anandiopsa ine; ndipo mdzakazi wanu ndinati, Ndilankhuletu ndi mfumu; kapena mfumu idzachita chopempha mdzakazi wake.
2 Samueli 14:16 - Buku Lopatulika Pakuti mfumu idzamvera ndi kupulumutsa mdzakazi wake m'dzanja la munthu wakufuna kundiononga ine pamodzi ndi mwana wanga, kutichotsa ku cholowa cha Mulungu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pakuti mfumu idzamvera ndi kupulumutsa mdzakazi wake m'dzanja la munthu wakufuna kundiononga ine pamodzi ndi mwana wanga, kutichotsa ku cholowa cha Mulungu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ndimaganiza kuti inu amfumu mutazimva, mudzandipulumutsa kwa munthu amene afuna kundiwononga ine pamodzi ndi mwana wanga, potero nkutichotsa pa kadziko kathu kamene adatipatsa Mulungu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwina mfumu idzavomereza kupulumutsa mdzakazi wake mʼdzanja la munthu amene akufuna kupha ine pamodzi ndi mwana wanga kutichotsa pa cholowa chimene Mulungu anatipatsa.’ |
Chifukwa chake tsono chakuti ndadzanena mau awa ndi mbuye wanga mfumu, ndicho kuti anthu anandiopsa ine; ndipo mdzakazi wanu ndinati, Ndilankhuletu ndi mfumu; kapena mfumu idzachita chopempha mdzakazi wake.
Ine ndine wa awo amene ali amtendere ndi okhulupirika mu Israele; inu mulikufuna kuononga mzinda ndi mai wa mu Israele; mudzamezeranji cholowa cha Yehova?
Chifukwa chake mbuye wanga mfumu amvere mau a kapolo wake. Ngati ndi Yehova anakuutsirani inu kutsutsana ndi ine, alandire chopereka; koma ngati ndi ana a anthu, atembereredwe pamaso pa Yehova, pakuti anandipirikitsa lero kuti ndisalandireko cholowa cha Yehova, ndi kuti, Muka, utumikire milungu ina.